1
YOHANE 5:24
Buku Lopatulika
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo.
နှိုင်းယှဉ်
YOHANE 5:24ရှာဖွေလေ့လာလိုက်ပါ။
2
YOHANE 5:6
Yesu, pakuona ameneyo alikugona, ndipo anadziwa kuti anatero nthawi yaikulu pamenepo, ananena naye, Ufuna kuchiritsidwa kodi?
YOHANE 5:6ရှာဖွေလေ့လာလိုက်ပါ။
3
YOHANE 5:39-40
Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo; ndipo simufuna kudza kwa Ine, kuti mukhale nao moyo.
YOHANE 5:39-40ရှာဖွေလေ့လာလိုက်ပါ။
4
YOHANE 5:8-9
Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende. Ndipo pomwepo munthuyu anachira, nayalula mphasa yake, nayenda. Koma tsiku lomwelo linali la Sabata.
YOHANE 5:8-9ရှာဖွေလေ့လာလိုက်ပါ။
5
YOHANE 5:19
Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu ndinena kwa inu, sangathe Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo.
YOHANE 5:19ရှာဖွေလေ့လာလိုက်ပါ။
ပင်မစာမျက်နှာ
သမ္မာကျမ်းစာ
အစီအစဉ်များ
ဗီဒီယိုများ