1
Yoh. 10:10
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
Jämför
Utforska Yoh. 10:10
2
Yoh. 10:11
“Ine ndine mbusa wabwino. Mbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.
Utforska Yoh. 10:11
3
Yoh. 10:27
Nkhosa zanga zimamva mau anga. Ine ndimazidziŵa, ndipo zimanditsatira.
Utforska Yoh. 10:27
4
Yoh. 10:28
Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga.
Utforska Yoh. 10:28
5
Yoh. 10:9
Khomo ndine. Munthu akaloŵera pa Ine, adzapulumuka. Azidzaloŵa ndi kutuluka, ndipo adzapeza chakudya.
Utforska Yoh. 10:9
6
Yoh. 10:14
Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziŵa, ndipo izozo Ineyo zimandidziŵa
Utforska Yoh. 10:14
7
Yoh. 10:29-30
Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo palibe amene angathe kuzilanda m'manja mwao. Ine ndi Atate ndife amodzi.”
Utforska Yoh. 10:29-30
8
Yoh. 10:15
monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo.
Utforska Yoh. 10:15
9
Yoh. 10:18
Palibe munthu wondilanda moyo wangawu, koma ndikuupereka ndekha. Ndili nazo mphamvu zoutaya moyo wanga, ndili nazonso mphamvu zoutenganso. Udindo umenewu ndidaulandira kwa Atate anga.”
Utforska Yoh. 10:18
10
Yoh. 10:7
Tsono Yesu adatinso, “Ndithu ndikunenetsa kuti Ine ndine khomo la nkhosa.
Utforska Yoh. 10:7
11
Yoh. 10:12
Koma wolembedwa ntchito chabe akaona mmbulu ulikudza, amazisiya nkhosazo iye nkuthaŵa. Amatero popeza kuti si mbusa weniweni, ndipo nkhosa si zake ai. Tsono mmbulu uja umagwirapo zina, zina nkumwazikana.
Utforska Yoh. 10:12
12
Yoh. 10:1
“Kunena zoona, munthu woloŵa m'khola la nkhosa osadzera pa khomo, koma kuchita kukwerera pena, ameneyo ndi wakuba ndi wolanda.
Utforska Yoh. 10:1
Hem
Bibeln
Planer
Videor