GENESIS 13
13
Abramu ndi Loti alekana
1Ndipo anakwera Abramu kuchoka ku Ejipito, iye ndi mkazi wake, ndi zonse anali nazo, ndi Loti pamodzi naye, kunka ku dziko la kumwera. 2Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng'ombe ndi siliva ndi golide. 3#Gen. 12.8Ndipo anankabe ulendo wake kuchokera ku dziko la kumwera kunka ku Betele, kufikira kumalo kumene kunali hema wake poyamba paja pakati pa Betele ndi Ai; 4#Gen. 12.8kumalo kwa guwa la nsembe analimanga iye kumeneko, poyamba paja; ndipo pamenepo Abramu anaitanira dzina la Yehova. 5Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi mahema. 6Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chao chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi. 7Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti: Akanani ndi Aperizi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m'dzikomo. 8Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale. 9#Gen. 20.15Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere. 10Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari. 11Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake. 12Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'midzi ya m'chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu. 13#Gen. 18.20Ndipo anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.
Mulungu alonjeza kwa Abramu kumpatsa Kanani
14Ndipo Yehova anati kwa Abramu, atalekana naye Loti, Tukulatu maso ako, nuyang'anire kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kumwera, ndi kum'mawa, ndi kumadzulo: 15#Gen. 17.8; 28.13; 35.12; Mac. 7.5chifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbeu yako nthawi yonse. 16#Gen. 10.22; Aro. 4.17-18; Aheb. 11.12Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa. 17Tauka, nuyendeyende m'dzikoli m'litali mwake ndi m'mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo. 18#Gen. 14.13Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure, imene ili m'Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.
Nu markerat:
GENESIS 13: BLPB2014
Märk
Dela
Kopiera
Vill du ha dina höjdpunkter sparade på alla dina enheter? Registrera dig eller logga in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: