Gen. 2
2
1Motero dziko lonse lapansi, thambo ndi zonse zokhala m'menemo, zidatha kulengedwa. 2#Eks. 20.11#Ahe. 4.4, 10 Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi Mulungu adamaliza ntchito imene ankachitayo, ndipo adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. 3Mulungu adadalitsa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, naliyeretsa, chifukwa choti pa tsiku limenelo adapuma atatsiriza zonse zimene ankachita. 4Ndimo m'mene dziko lapansi ndi zonse zakuthambo zidalengedwera.
Munda wa Edeni
Pamene Chauta ankalenga dziko lapansi ndi zonse zakuthambo, 5panalibe chomera chilichonse pa dziko lapansi, ndipo mbeu zinali zisanamere, chifukwa Chauta Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Ndipo panalibenso wina aliyense wolima pa nthaka. 6Koma madzi ankatuluka m'dziko lonse lapansi ndi kumathirira nthaka. 7#Lun. 15.8, 11; 1Ako. 15.45 Tsono Chauta adatenga dothi#2.7: dothi…munthu: M'chihebri mau ameneŵa amamveka chimodzimodzi. pa nthaka, ndipo adaumba munthu ndi dothilo. Adamuuzira mpweya wopatsa moyo m'mphuno zake, ndipo munthuyo adakhala wamoyo. 8Kenaka Chauta adatsekula munda mu Edeni chakuvuma, ndipo munthu adamuumbayo adamkhazika m'menemo. 9#Chiv. 2.7; 22.2, 14 Chauta adameretsamo mitengo yokongola ya zipatso zokoma. Pakati pa mundawo panali mtengo wopatsa moyo, ndiponso mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa.
10Mtsinje wotuluka mu Edeni momwemo, unkayenda numathirira mundawo. Mtsinjewo udagaŵika panai, nusanduka mitsinje inai. 11Mtsinje woyamba ndi Pisoni, ndipo umayenda mozungulira dziko la Havila, kumene kumapezeka golide. 12(Golide wakumeneko ndi wabwino. Kumapezekanso bedeliyo ndi miyala ya mtengowapatali yotchedwa onikisi.) 13Mtsinje wachiŵiri ndi Gihoni, ndipo umayenda mozungulira dziko la Kusi. 14Mtsinje wachitatu ndi Tigrisi, umene umayenda kuvuma kwa Asiriya. Mtsinje wachinai ndi Yufurate.
15Tsono Chauta adamtenga munthuyo, namukhazika m'munda wa Edeni uja kuti azilima ndi kumausamala. 16Ndipo Chauta adamlamula munthuyo kuti, “Uzidya zipatso za mtengo uliwonse wam'mundawu, 17kupatula mtengo wokhawo umene umadziŵitsa zabwino ndi zoipa. Zipatso za mtengo umenewo usadye. Ukadzadya, ndithu udzafa!”
18Pambuyo pake Chauta adati, “Sibwino kuti munthuyu akhale yekha. Ndipanga mnzake woti azimthandiza.” 19Chauta adatenga dothi naumba nyama zonse ndi mbalame zonse, nabwera nazo kwa Adamu kuti azitche maina. Mwakuti maina amene Adamu adazitcha, maina ake ndi omwewo. 20Adamu adazitcha maina nyama zonse, mbalame ndi zamoyo zonse zakuthengo. Komabe panalibe mnzake woti azimthandiza. 21Tsono Chauta adagonetsa Adamu tulo tofanato, ndipo ali m'tulo choncho, Mulungu adamchotsako nthiti, natsekapo ndi mnofu pamalopo. 22Chauta Mulungu adapanga mkazi ndi nthiti imene adaichotsa kwa Adamu uja, ndipo mkaziyo Mulungu adabwera naye kwa iye.
23Adamu adati,
“Uyutu ndiye ndi fupa lochokera ku mafupa anga,
mnofu wochokera ku mnofu wanga.
Adzatchedwa Mkazi,
chifukwa watengedwa kwa Mwamuna.”
24 #
Mt. 19.5; Mk. 10.7, 8; 1Ako. 6.16; Aef. 5.31 Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho aŵiriwo amakhala thupi limodzi. 25Mwamunayo ndi mkazi wake uja, onse anali maliseche, komabe sankachita manyazi.
Bible Society of Malawi