GENESIS 4
4
Kaini ndi Abele. Kuphedwa koyamba
1Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova. 2Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka. 3#Lev. 2.12Ndipo panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova. 4#Eks. 13.12; Aheb. 11.4Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang'anira Abele ndi nsembe yake: 5koma sanayang'anire Kaini ndi nsembe yake. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yake. 6Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako? 7#Aro. 2.6-11Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye. 8#1Yoh. 3.12Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwake. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha. 9#Yoh. 8.44Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang'anira mphwanga? 10#Aheb. 12.24Ndipo anati, Wachita chiyani? Mau a mwazi wa mphwako andifuulira Ine kunthaka. 11Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira pa dzanja lako mwazi wa mphwako: 12pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi. 13Ndipo Kaini anati kwa Yehova, Kulangidwa kwanga nkwakukulu kosapiririka. 14#Mas. 51.11Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha. 15#Ezk. 9.4, 6Ndipo Yehova anati kwa iye, Chifukwa chake aliyense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika chizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe aliyense akampeza.
Mbumba ya Kaini
16Ndipo Kaini anatuluka pamaso pa Yehova, ndipo anakhala m'dziko la Nodi, kum'mawa kwake kwa Edeni. 17Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoki: ndipo anamanga mudzi, nautcha dzina lake la mudziwo monga dzina la mwana wake, Enoki. 18Kwa Enoki ndipo kunabadwa Iradi; Iradi ndipo anabala Mehuyaele; Mehuyaele ndipo anabala Metusaele; Metusaele ndipo anabala Lameki. 19Ndipo Lameki anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila. 20Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wao wa iwo okhala m'mahema, akuweta ng'ombe. 21Ndi dzina la mphwake ndilo Yubale; iye ndiye atate wao wa iwo oimba zeze ndi chitoliro. 22Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a chitsulo; mlongo wake wa Tubala-Kaini ndi Naama. 23Lameki ndipo anati kwa akazi ake,
Tamvani mau anga, Ada ndi Zila;
inu akazi a Lameki, mverani kunena kwanga:
Ndapha munthu wakundilasa ine,
ndapha mnyamata wakundipweteka ine.
24Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kawiri,
koma Lameki makumi asanu ndi awiri.
Kubadwa kwa Seti
25Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti: Chifukwa, nati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha. 26#Mas. 116.17; Zef. 3.6; Zek. 13.9Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwa mwana wamwamuna: anamutcha dzina lake Enosi: pomwepo anthu anayamba kutchula dzina la Yehova.
Currently Selected:
GENESIS 4: BLPB2014
ማድመቅ
Share
Copy
ያደመቋቸው ምንባቦች በሁሉም መሣሪያዎችዎ ላይ እንዲቀመጡ ይፈልጋሉ? ይመዝገቡ ወይም ይግቡ
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi