1
GENESIS 37:5
Buku Lopatulika
Yosefe ndipo analota loto, nawafotokozera abale ake; ndipo anamuda iye koposa.
Compare
Explore GENESIS 37:5
2
GENESIS 37:3
Koma Israele anamkonda Yosefe koposa ana ake onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wake; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro.
Explore GENESIS 37:3
3
GENESIS 37:4
Ndipo abale ake anaona kuti atate wake anamkonda iye koposa abale ake onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.
Explore GENESIS 37:4
4
GENESIS 37:9
Ndipo analotanso loto lina, nafotokozera abale ake, nati, Taonani, ndalotanso loto lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine.
Explore GENESIS 37:9
5
GENESIS 37:11
Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake.
Explore GENESIS 37:11
6
GENESIS 37:6-7
Ndipo iye anati kwa iwo, Tamvanitu loto limene ndalota: pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m'munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima chilili! Ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga.
Explore GENESIS 37:6-7
7
GENESIS 37:20
Tiyeni tsopano timuphe iye timponye m'dzenje, ndipo tidzati, Wajiwa ndi chilombo; ndipo tidzaona momwe adzachita maloto ake.
Explore GENESIS 37:20
8
GENESIS 37:28
Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.
Explore GENESIS 37:28
9
GENESIS 37:19
Ndipo anati wina ndi mnzake, Taonani, alinkudza mwini maloto uja.
Explore GENESIS 37:19
10
GENESIS 37:18
Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe.
Explore GENESIS 37:18
11
GENESIS 37:22
Ndipo Rubeni anati kwa iwo, Musakhetse mwazi; mponyeni iye m'dzenjemo m'chipululu muno, koma musamsamulire iye manja: kuti ampulumutse iye m'manja mwao, ambwezenso kwa atate wake.
Explore GENESIS 37:22
Home
Bible
Plans
Videos