GENESIS 37
37
Yosefe agulitsidwa ndi abale ake
1 #
Gen. 36.7; Aheb. 11.9 Ndipo Yakobo anakhala m'dziko limene anakhalamo mlendo atate wake, m'dziko la Kanani. 2Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana aamuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa. 3Koma Israele anamkonda Yosefe koposa ana ake onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wake; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro. 4#Gen. 49.23Ndipo abale ake anaona kuti atate wake anamkonda iye koposa abale ake onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere. 5Yosefe ndipo analota loto, nawafotokozera abale ake; ndipo anamuda iye koposa. 6Ndipo iye anati kwa iwo, Tamvanitu loto limene ndalota: 7pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m'munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima chilili! Ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga. 8Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake. 9Ndipo analotanso loto lina, nafotokozera abale ake, nati, Taonani, ndalotanso loto lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine. 10Ndipo iye anafotokozera atate wake ndi abale ake; ndipo atate wake anamdzudzula, nati kwa iye, Loto limene walota iwe nlotani? Kodi ine ndi amai ako ndi abale ako tidzafika ndithu tokha kuweramira iwe pansi? 11#Luk. 2.19; Mac. 7.9Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake. 12Ndipo abale ake ananka kukaweta zoweta za atate wao mu Sekemu. 13Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Kodi abale ako sadyetsa zoweta mu Sekemu? Tiyeni, ndikutuma iwe kwa iwo. Ndipo anati, Ndine pano. 14Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta zili bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kuchokera m'chigwa cha Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu. 15Ndipo anampeza munthu, taonani, analinkusokera m'thengo; munthuyo ndipo anamfunsa, nati, Kodi ufuna chiyani? 16Ndipo iye anati, Ndifuna abale anga. Undiuzetu kumene adyetsa zoweta. 17#2Maf. 6.13Munthuyo ndipo anati, Anachoka pano; pakuti ndinamva alinkuti, Timuke ku Dotani. Yosefe ndipo anatsata abale ake, nawapeza ali ku Dotani. 18#Mas. 37.12, 32Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe. 19Ndipo anati wina ndi mnzake, Taonani, alinkudza mwini maloto uja. 20Tiyeni tsopano timuphe iye timponye m'dzenje, ndipo tidzati, Wajiwa ndi chilombo; ndipo tidzaona momwe adzachita maloto ake. 21#Gen. 42.22Ndipo Rubeni anamva nampulumutsa iye m'manja mwao; nati, Tisamuphe iye. 22Ndipo Rubeni anati kwa iwo, Musakhetse mwazi; mponyeni iye m'dzenjemo m'chipululu muno, koma musamsamulire iye manja: kuti ampulumutse iye m'manja mwao, ambwezenso kwa atate wake. 23Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ake, anamvula Yosefe malaya ake, malaya amwinjiro amene anavala iye; 24#Yer. 38.6ndipo anamtenga iye, namponya m'dzenjemo; m'dzenjemo munalibe kanthu, munalibe madzi m'menemo. 25Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndi ngamira zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi mure alinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito. 26Ndipo Yuda anati kwa abale ake, Nanga tidzapindulanji tikamupha mbale wathu ndi kufotsera mwazi wake? 27#1Sam. 18.17Tiyeni timgulitse iye kwa Aismaele, tisasamulire iye manja; chifukwa ndiye mbale wathu, thupi lathu. Ndipo anamvera iye abale ake. 28#Mas. 105.17; Mac. 7.9Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.
29 #
Num. 14.6; 2Sam. 1.11; Mat. 26.65 Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m'dzenjemo: ndipo iye anang'amba nsalu yake. 30Ndipo anabwera kwa abale ake, nati, Mwana palibe; ndipo ine ndipita kuti? 31Ndipo anatenga malaya ake a Yosefe, napha tonde, naviika malaya m'mwazi wake: 32natumiza malaya amwinjiro, nadza nao kwa atate ao: ndipo anati, Siwa tawatola; muzindikire tsono ngati ndi malaya a mwana wanu, kapena ndi ena. 33Ndipo anazindikira nati, Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi chilombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu. 34Yakobo ndipo anang'amba malaya ake, na vala chiguduli m'chuuno mwake namlirira mwana wake masiku ambiri. 35#2Sam. 12.17Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira. 36Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.
Currently Selected:
GENESIS 37: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi