GENESIS 36
36
Mbumba ya Esau
(1Mbi. 1.34-37)
1 #
1Mbi. 1.35
Mibadwo ya Esau (ndiye Edomu) ndi iyi: 2Esau anatenga akazi ake a ana aakazi a mu Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Muhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni Muhivi; 3ndi Basemati mwana wamkazi wa Ismaele, mlongo wake wa Nebayoti. 4Ndipo Ada anambalira Esau Elifazi; ndipo Basemati anabala Reuwele; 5ndipo Oholibama anabala Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora; amenewa ndi ana aamuna a Esau, amene anambadwira m'dziko la Kanani. 6Ndipo Esau anatenga akazi ake, ndi ana ake aamuna, ndi ana ake aakazi, ndi anthu onse a m'banja mwake, ndi ng'ombe zake, ndi zoweta zake, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m'dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patali ndi Yakobo mphwake. 7Chifukwa chuma chao chinali chambiri chotero kuti sanakhoze kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoze kuwakwanira chifukwa cha ng'ombe zao. 8#Yos. 24.4Ndipo Esau anakhala m'phiri la Seiri; Esau ndiye Edomu. 9Mibadwo ya Esau atate wao wa Aedomu m'phiri la Seiri ndi iyi: 10amenewa ndi maina a ana aamuna a Esau: Elifazi mwana wamwamuna wa Ada, mkazi wake wa Esau, Reuwele mwana wamwamuna wa Basemati mkazi wake wa Esau. 11Ndipo ana aamuna a Elifazi ndiwo Temani, Omara, Zefo ndi Gatamu, ndi Kenazi. 12Ndipo Timna anali mkazi wake wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleke: amenewa ndi ana aamuna a Ada mkazi wake wa Esau. 13Ndi ana aamuna a Reuwele: Nahati, ndi Zera, Sama, ndi Miza; amenewa ndi ana a Basemati mkazi wake wa Esau. 14Ana aamuna a Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni, mkazi wake wa Esau, ndi awa: ndipo iye anambalira Esau Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora. 15Amenewa ndi mafumu a ana aamuna a Esau: ana aamuna a Elifazi woyamba wa Esau: mfumu Temani, mfumu Omara, mfumu Zefo, mfumu Kenazi, 16mfumu Kora, mfumu Gatamu, mfumu Amaleke: amenewa ndi mafumu a kwa Elifazi m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana aamuna a Ada. 17Amenewa ndi ana aamuna a Reuwele mwana wamwamuna wa Esau: mfumu Nahati, mfumu Zera, mfumu Sama, mfumu Miza; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Reuwele m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana aamuna a Basemati mkazi wake wa Esau. 18Amenewa ndi ana aamuna a Oholibama mkazi wake wa Esau; mfumu Yeusi, mfumu Yalamu, mfumu Kora, amenewa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wake wa Esau. 19Amenewa ndi ana aamuna a Esau, amenewa ndi mafumu ao; yemweyo ndi Edomu.
20Amenewa ndi ana aamuna a Seiri Muhori, okhala m'dzikomo: Lotani ndi Sobala, ndi Zibiyoni, ndi Ana, 21ndi Disoni ndi Ezere ndi Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, ana a Seiri, m'dziko la Edomu. 22Ndi ana a Lotani anali Hori ndi Hemani: mlongo wake wa Lotani anali Timna. 23Ana a Sobala ndi awa: Alivani ndi Manahati ndi Ebala, Sefo ndi Onamu. 24Ana a Zibiyoni ndi amenewa: Aiya ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'chipululu, pakudyetsa abulu a Zibiyoni atate wake. 25Ana a Ana ndi awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana. 26Ana a Disoni ndi awa: Hemudani ndi Esibani ndi Itirani, ndi Kerani. 27Ana a Ezere ndi awa: Bilihani, ndi Zaavani, ndi Akani. 28Ana a Disani ndi awa: Uzi ndi Arani. 29Mafumu obadwa kwa Ahori: mfumu Lotani, mfumu Sobala, mfumu Zibiyoni, mfumu Ana, 30mfumu Disoni, mfumu Ezere, mfumu Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, monga mwa maufumu ao m'dziko la Seiri.
31 #
1Mbi. 1.43
Amenewa ndi mafumu analamulira m'dziko la Edomu, asadalamulire ana a Israele mfumu aliyense. 32Ndipo Bela mwana wamwamuna wa Beori, analamulira mu Edomu, ndipo dzina la mzinda wake ndilo Dinihaba. 33Ndipo Bela anamwalira, ndipo Yobabu mwana wamwamuna wa Zera wa ku Bozira analamulira m'malo mwake. 34Ndipo Yobabu anamwalira, ndipo Husamu wa ku dziko la Atemani analamulira m'malo mwake. 35Ndipo Husamu anamwalira, ndipo Hadadi mwana wamwamuna wa Bedadi, amene anakantha Midiyani m'dambo la Mowabu, analamulira m'malo mwake: dzina la mzinda wake ndi Aviti. 36Ndipo Hadadi anamwalira, ndipo Samila wa ku Masireka analamulira m'malo mwake. 37Ndipo Samila anamwalira, ndipo Shaulo wa ku Rehoboti pambali pa nyanja analamulira m'malo mwake. 38Ndipo Shaulo anamwalira, ndipo Baala-Hanani mwana wamwamuna wa Akibori analamulira m'malo mwake. 39Ndipo Baala-Hanani mwana wamwamuna wa Akibori anamwalira, ndipo Hadari analamulira m'malo mwake; dzina la mzinda wake ndi Pau; ndipo dzina la mkazi wake ndi Mehetabele, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Mezahabu. 40#1Mbi. 1.51Maina a mafumu obadwa kwa Esau, monga mabanja ao, monga malo ao, monga maina ao ndi awa: mfumu Timna, mfumu Aliva, mfumu Yeteti, 41mfumu Oholibama, mfumu Ela, mfumu Pinoni, 42mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mibizara, 43mfumu Magadiele, mfumu Iramu; amenewa ndi mafumu a Edomu, monga mwa kukhala kwao m'dziko lokhala laolao. Uyo ndiye Esau atate wao wa Aedomu.
Currently Selected:
GENESIS 36: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi