GENESIS 35
35
Yakobo amanga ku Betele
1 #
Gen. 28.12
Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Betele nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako. 2#Eks. 19.10; Yos. 24.23; 1Sam. 7.3Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo ili mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu: 3#Gen. 32.7, 24tinyamuke, tikwere tinke ku Betele: ndipo tidzamanga kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anandivomereza tsiku la mavuto anga, ndiponso anali ndi ine m'njira m'mene ndinapitamo. 4Ndipo anampatsa Yakobo milungu yachilendo yonse inali m'manja mwao, ndi mphete zinali m'makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu. 5#Eks. 15.16; 23.27Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera mizinda yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo. 6Ndipo Yakobo anafika ku Luzi, ndiko ku dziko la Kanani (ndiwo Betele), iye ndi anthu onse anali pamodzi ndi iye. 7#Gen. 35.1Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, natcha pamenepo El Betele: pakuti kumeneko Mulungu anaonekera kwa iye muja anathawa pa nkhope ya mbale wake. 8Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Betele, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anatcha dzina lake Aloni-Bakuti.
9Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anachokera mu Padanaramu, namdalitsa iye. 10#Gen. 32.28Ndipo Mulungu anati kwa iye, Dzina lako ndi Yakobo; dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma dzina lako lidzakhala Israele: ndipo anamutcha dzina lake Israele. 11#Gen. 48.3-4Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m'chuuno mwako; 12ndipo dziko limene ndinapatsa kwa Abrahamu ndi kwa Isaki ndidzalipatsa kwa iwe ndipo ndidzapatsa mbeu zako za pambuyo pako dzikoli. 13Ndipo Mulungu anakwera kumchokera iye kumene ananena naye. 14#Gen. 28.18Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamalo pamene ananena ndi iye, choimiritsa chamwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta. 15Ndipo Yakobo anatcha dzina lake la pamalo pamene Mulungu ananena ndi iye, Betele.
Rakele amwalira pobadwa Benjamini
16Ndipo anachokera ku Betele: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efurata: ndipo Rakele anabala navutidwa. 17Ndipo panali pamene anavutidwa, namwino anati kwa iye, Usaope: pakuti udzakhala ndi mwana wina wamwamuna. 18Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamutcha dzina lake Benoni; koma atate wake anamutcha Benjamini. 19#Gen. 48.7Ndipo anafa Rakele, naikidwa panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu). 20Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamanda pake: umenewo ndi choimiritsa cha pa manda a Rakele kufikira lero. 21Ndipo Israele anapita namanga hema wake paseri pa nsanja ya Edere.
Ana a Yakobo
(1Mbi. 2.1-2)
22Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri: 23ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara; 24ana aamuna a Rakele: ndiwo Yosefe ndi Benjamini; 25ana aamuna a Biliha mdzakazi wake wa Rakele: ndiwo Dani ndi Nafutali; 26ndipo ana aamuna a Zilipa mdzakazi wake wa Leya: ndiwo Gadi ndi Asere: amenewo ndi ana aamuna a Yakobo amene anabala iye mu Padanaramu.
Imfa ya Isaki
27Ndipo Yakobo anafika kwa Isaki atate wake ku Mamure, ku Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni) kumene anakhala Abrahamu ndi Isaki. 28Ndipo masiku a Isaki anali zaka zana limodzi kudza makumi asanu ndi atatu. 29Ndipo Isaki anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake aamuna anamuika iye.
Currently Selected:
GENESIS 35: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi