1
Yohane 14:27
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.
Compare
Explore Yohane 14:27
2
Yohane 14:6
Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.
Explore Yohane 14:6
3
Yohane 14:1
“Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso.
Explore Yohane 14:1
4
Yohane 14:26
Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani.
Explore Yohane 14:26
5
Yohane 14:21
Iye amene amadziwa malamulo anga ndi kuwasunga ndiye amene amandikonda. Wokonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga ndipo Inenso ndidzamukonda ndikudzionetsa ndekha kwa iye.”
Explore Yohane 14:21
6
Yohane 14:16-17
Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse. Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu.
Explore Yohane 14:16-17
7
Yohane 14:13-14
Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita.
Explore Yohane 14:13-14
8
Yohane 14:15
“Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga.
Explore Yohane 14:15
9
Yohane 14:2
Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo.
Explore Yohane 14:2
10
Yohane 14:3
Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko.
Explore Yohane 14:3
11
Yohane 14:5
Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye ife sitikudziwa kumene Inu mukupita, nanga tingadziwe bwanji njirayo?”
Explore Yohane 14:5
Home
Bible
Plans
Videos