Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anatulukira kukazonda abale ake, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu Mwejipito ali kukantha Muhebri, wa abale ake. Ndipo anaunguza kwina ndi kwina, ndipo pamene anaona kuti palibe munthu, anakantha Mwejipito, namfotsera mumchenga.