Koma uta wake unakhala wamphamvu,
ndi mikono ya manja ake inalimbitsidwa.
Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo.
(Kuchokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israele,)
Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe,
ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe.
Ndi madalitso a Kumwamba,
madalitso a madzi akuya akukhala pansi,
madalitso a mawere, ndi a mimba.