1
AROMA 14:17-18
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera. Pakuti iye amene atumikira Khristu mu izi akondweretsa Mulungu, navomerezeka ndi anthu.
Compare
Explore AROMA 14:17-18
2
AROMA 14:8
Pakuti tingakhale tili ndi moyo, tikhalira Ambuye moyo; kapena tikafa, tifera Ambuye; chifukwa chake tingakhale tili ndi moyo, kapena tikafa, tikhala ake a Ambuye.
Explore AROMA 14:8
3
AROMA 14:19
Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.
Explore AROMA 14:19
4
AROMA 14:13
Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa pa njira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa.
Explore AROMA 14:13
5
AROMA 14:11-12
Pakuti kwalembedwa, Pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malilime onse adzavomereza Mulungu. Chotero munthu aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu.
Explore AROMA 14:11-12
6
AROMA 14:1
Ndipo iye amene ali wofooka m'chikhulupiriro, mumlandire, koma si kuchita naye makani otsutsana ai.
Explore AROMA 14:1
7
AROMA 14:4
Ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wake? Iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuimiritsa.
Explore AROMA 14:4
Home
Bible
Plans
Videos