EKSODO 1
1
Masautso a ana a Israele mu Ejipito
1 #
Gen. 46.8
Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa mu Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake: 2Rubeni, Simeoni, Levi ndi Yuda; 3Isakara, Zebuloni, ndi Benjamini; 4Dani ndi Nafutali, Gadi ndi Asere. 5#Gen. 46.27Ndipo amoyo onse amene anatuluka m'chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; koma Yosefe anali mu Ejipito. 6Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ake onse, ndi mbadwo uwo wonse. 7#Deut. 26.5; Mac. 7.17Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.
8Pamenepo inalowa mfumu yatsopano mu ufumu wa Ejipito, imene siinadziwe Yosefe. 9#Mas. 105.24Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu. 10#Mac. 7.19Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo. 11#Gen. 15.13; 47.11Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi. 12Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele. 13Ndipo Aejipito anawagwiritsa ana a Israele ntchito yosautsa; 14nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.
Anamwino samvera mfumu
15Ndipo mfumu ya Aejipito inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lake la wina ndiye Sifira, dzina la mnzake ndiye Puwa; 16ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo. 17#Miy. 16.6Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana aamuna akhale ndi moyo. 18Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana aamunawo akhale ndi moyo? 19Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino. 20#Yes. 3.10Potero Mulungu anawachitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu. 21Ndipo kunatero kuti, popeza anamwino anaopa Mulungu, Iye anawamangitsira mabanja. 22#Mac. 7.19Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.
Currently Selected:
EKSODO 1: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi