GENESIS 22
22
Isaki aperekedwa nsembe
1 #
1Ako. 10.13; Aheb. 11.17; Yak. 1.12 Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano. 2Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isaki, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe. 3Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye. 4Tsiku lachitatu Abrahamu anatukula maso ake naona malowo patali. 5Ndipo Abrahamu anati kwa anyamata ake, Khalani kuno ndi bulu, ine ndi mwanayu tinka uko, ndipo tikapemphera ndi kubweranso kwa inu. 6#Yoh. 19.17Ndipo Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza, nazisenzetsa Isaki mwana wake; natenga moto m'dzanja lake ndi mpeni; nayenda pamodzi onse awiri. 7Ndipo Isaki ananena ndi Abrahamu atate wake, nati, Atate wanga; ndipo iye anati, Ndine pano, mwana wanga. Ndipo anati, Taonani moto ndi nkhuni; koma mwanawankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti? 8#Yoh. 1.29Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwanawankhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri. 9Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isaki mwana wake, namuika iye paguwa la nsembe pamwamba pa nkhuni. 10Ndipo Abrahamu anatambasula dzanja lake, natenga mpeni kuti amuphe mwana wake. 11Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano. 12Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha. 13Ndipo Abrahamu anatukula maso ake nayang'ana taonani, pambuyo pake nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zake m'chiyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake. 14Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka. 15Ndipo mthenga wa Yehova anamuitana Abrahamu ndi mau odzera kumwamba kachiwiri, 16#Luk. 1.73; Aheb. 6.13nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikanize mwana wako, mwana wako yekha, 17#Yer. 33.22kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao; 18#Gen. 12.3; 18.18; 24.4-5; Agal. 3.8m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mau anga. 19Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ake, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba.
20 #
Gen. 11.29
Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Taonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana; 21Uzi woyamba ndi Buzi mphwake, ndi Kemuwele atate wake wa Aramu; 22ndi Kesedi, ndi Hazo, ndi Pilidasi ndi Yidilafi, ndi Betuele. 23#Gen. 24.15Ndimo Betuele anabala Rebeka: amenewa asanu ndi atatu Milika anambalira Nahori mphwake wa Abrahamu. 24Ndipo mkazi wake wamng'ono, dzina lake Reuma, iyenso anabala Teba, ndi Gahamu, ndi Tahasi, ndi Maaka.
Currently Selected:
GENESIS 22: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi