GENESIS 25
25
Kumwalira kwa Abrahamu
(1Mbi. 1.32-33)
1Ndipo Abrahamu anatenga mkazi wina dzina lake Ketura. 2Ndipo anambalira iye Zimirani ndi Yokisani ndi Medani, ndi Midiyani, ndi Isibaki, ndi Suwa. 3Ndipo Yokisani anabala Sheba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi. 4Ana a Midiyani: Efa, ndi Efere, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elida. Onse amenewa ndi ana a Ketura. 5#Gen. 24.36Ndipo Abrahamu anampatsa Isaki zonse anali nazo. 6Koma kwa ana a akazi ake aang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawachotsa iwo kwa Isaki mwana wake, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa. 7Masiku a zaka za moyo wake wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu. 8#Gen. 35.29Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa mu ukalamba wake wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wake. 9Ndipo ana ake Isaki ndi Ismaele anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efuroni mwana wake wa Zohari Muhiti, umene uli patsogolo pa Mamure; 10#Gen. 49.30-31munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Hiti. Pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake. 11Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isaki mwana wake; ndipo Isaki anakhala pa Beere-Lahai-Roi.
Mbumba ya Ismaele
(1Mbi. 1.28-31)
12Mibadwo ya Ismaele mwana wamwamuna wa Abrahamu, amene Hagara Mwejipito mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi: 13ndipo maina a ana a Ismaele, maina ao m'mibadwo yao ndi awa: woyamba wa Ismaele ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Adibeele, ndi Mibisamu, 14ndi Misima, ndi Duma, ndi Masa; 15ndi Hadadi, ndi Tema, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Kedema; 16ana a Ismaele ndi awa: maina ao m'midzi yao, m'misasa yao ndi awa: akalonga khumi ndi awiri m'mitundu yao. 17Zaka za moyo wa Ismaele ndi izi: zaka zana limodzi kudza makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri: ndipo iye anamwalira, natengedwa akhale ndi a mtundu wake. 18Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwake kwa Ejipito, pakunka ku Asiriya: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ake onse.
Esau ndi Yakobo
19Mibadwo ya Isaki mwana wake wa Abrahamu ndi iyi: Abrahamu anabala Isaki: 20ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu. 21Ndipo Isaki anampembedzera mkazi wake kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwake, ndipo Rebeka mkazi wake anatenga pakati. 22Ndipo ana analimbana m'kati mwake: ndipo iye anati, Ngati chotero, ine ndikhala ndi moyo bwanji? Ndipo ananka kukafunsa kwa Yehova. 23#2Sam. 8.14; Aro. 9.12Yehova ndipo anati kwa iye,
Mitundu iwiri ili m'mimba mwako,
magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako;
gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake;
wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.
24Atatha masiku ake akubala, taonani, amapasa anali m'mimba mwake. 25Ndipo woyamba anabadwa wofiira, mwake monse monga malaya aubweya; ndipo anamutcha dzina lake Esau. 26#Hos. 12.3Pambuyo pake ndipo anabadwa mphwake ndipo dzanja lake linagwira chitendeni cha Esau, ndi dzina lake linatchedwa Yakobo: ndipo Isaki anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wake anabala iwo.
Esau agulitsa ukulu wake
27Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema. 28Ndipo Isaki anakonda Esau, chifukwa anadya nyama yake ya m'thengo; koma Rebeka anakonda Yakobo. 29Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anachokera kuthengo, nalefuka: 30ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye chofiiracho; chifukwa ndalefuka: chifukwa chake anamutcha dzina lake Edomu. 31Ndipo Yakobo anati, Tigulane lero ukulu wako. 32Ndipo Esau anati, Taona, ine ndifuna kufa: ukuluwo ndidzapindulanji nao? 33#Aheb. 12.16Ndipo anati Yakobo, Undilumbirire ine lero lomwe, ndipo analumbirira iye; nagulana ndi Yakobo ukulu wake. 34Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita: chomwecho Esau ananyoza ukulu wake.
Currently Selected:
GENESIS 25: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi