GENESIS 27
27
Yakobo adalitsidwa m'malo mwa Esau
1Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano. 2Ndipo anati, Taonatu, ndakalamba, sindidziwa tsiku la kufa kwanga: 3Tsopano tengatu zida zako ndi phodo lako ndi uta wako, numuke kuthengo kundisakira ine nyama: 4#Gen. 48.9; Deut. 33.1nundikonzere ine chakudya chokolera chonga chomwe ndichikonda ine, nudze nacho kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe. 5Ndipo anamva Rebeka pamene Isaki ananena ndi Esau mwana wake. Ndipo Esau ananka kuthengo kukasaka nyama ndi kubwera nayo. 6Ndipo Rebeka ananena kwa Yakobo mwana wake, nati, Taona ndinamva atate wako alimkunena ndi Esau mkulu wako kuti, 7Unditengere ine nyama, undikonzere ine chakudya chokolera, kuti ndidzadye, ndi kudalitsa iwe pamaso pa Yehova, ndisanafe. 8Tsopanotu mwana wanga, tamvera mau anga monga momwe nditi ndikuuze iwe. 9Pitatu kubusa, ukanditengere ine kumeneko tiana tiwiri tabwino tambuzi; ndikonzere nato chakudya chokolera cha atate wako chonga chomwe achikonda: 10ndipo udzapita nacho kwa atate wako, kuti adye, ndi kukudalitsa iwe asanafe. 11Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amake, Taonani, Esau mkulu wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu wosalala. 12#Deut. 27.18Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso. 13#1Sam. 25.24; Mat. 27.25Ndipo amake anati kwa iye, Pa ine likhale temberero lako mwana wanga; koma tamvera mau anga, kazimuka kunditengera timeneto. 14Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amake; amake ndipo anakonza chakudya chokolera chonga chimene anachikonda atate wake. 15Ndipo Rebeka anatenga zovala zokoma za Esau mwana wake wamkulu zinali m'nyumba, naveka nazo Yakobo mwana wake wamng'ono; 16ndipo anaveka zikopa za tiana tambuzi pamanja ake ndi pakhosi pake posalala; 17ndipo anapereka m'dzanja la mwana wake Yakobo chakudya chokoleracho, ndi mikate imene anaipanga. 18Ndipo iye analowa kwa atate wake, nati, Atate wanga; iye anati, Ndine pano; ndani iwe mwana wanga? 19Ndipo Yakobo anati kwa atate wake, Ndine Esau mwana wanu wamkulu; ndachita monga mwandiuza ine; ukanitu, khalani tsonga, idyani nyama yanga kuti moyo wanu undidalitse ine. 20Ndipo Isaki anati kwa mwana wake, Unaipeza msanga bwanji mwana wanga? Ndipo anati, Chifukwa kuti Yehova Mulungu wanu anandiyendetsa ine bwino. 21Ndipo Isaki anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina. 22Ndipo Yakobo anasendera kwa Isaki atate wake, ndipo anamyambasa nati, Mau ndi mau a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau. 23Ndipo sanamzindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye. 24Ndipo anati, Kodi ndiwe mwana wanga weniweni Esau? Ndipo anati, Ndine amene. 25Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye. 26Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga. 27#Hos. 14.6Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati,
Taona, kununkhira kwa mwana wanga,
kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;
28 #
Aheb. 11.20
Mulungu akupatse iwe mame a kumwamba,
ndi zonenepa za dziko lapansi,
ndi tirigu wambiri ndi vinyo.
29Anthu akutumikire iwe,
mitundu ikuweramire iwe;
uchite ufumu pa abale ako,
ana a amai ako akuweramire iwe.
Wotemberereka aliyense akutemberera iwe,
wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
30Ndipo panali atatha Isaki kumdalitsa Yakobo, atatuluka Yakobo pamaso pa Isaki atate wake, Esau mkulu wake analowa kuchokera kuthengo. 31Ndipo iyenso anakonza chakudya chokolera, nadza nacho kwa atate wake, nati kwa atate wake, Auke atate wanga, adye nyama ya mwana wake, kuti moyo wanu undidalitse ine. 32Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Ndiwe yani? Ndipo iye anati, Ndine mwana wanu woyamba Esau. 33Ndipo Isaki ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? Inde, adzadalitsika. 34Pamene Esau anamva mau a atate wake Isaki, analira ndi kulira kwakukulu ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wake, Mundidalitse ine, inenso atate wanga. 35Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako. 36Ndipo iye anati, Kodi si ndicho chifukwa anamutcha dzina lake Yakobo? Kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi simunandisungire ine mdalitso? 37Ndipo anayankha Isaki nati kwa Esau, Taona, ndamuyesa iye mkulu wako, ndi abale ake onse ndampatsa iye akhale akapolo ake; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakuchitira iwe chiyani? 38#Aheb. 12.16Ndipo Esau anati kwa atate wake, Kodi muli nao mdalitso umodzi wokha, atate wanga? Mundidalitse ine, inenso, atate wanga. Ndipo Esau anakweza mau ake nalira. 39Ndipo Isaki atate wake anayankha nati kwa iye,
Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi,
pa mame a kumwamba akudzera komwe.
40 #
2Maf. 8.20
Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako,
nudzakhala kapolo wa mphwako.
Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka,
udzachotsa goli lake pakhosi pako.
41 #
Gen. 50.3-4, 10 Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo. 42Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wake wamkulu: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wake wamng'ono, nati kwa iye, Taona, mkulu wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wake kuti adzakupha iwe. 43Ndipo tsopano mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harani; 44ukhale naye masiku akuwerengeka, mpaka utamchokera ukali mkulu wako; 45mpaka utamchokera mkwiyo mkulu wako, kuti aiwale chimene wamchitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi? 46Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?
Currently Selected:
GENESIS 27: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi