GENESIS 47
47
Yakobo aonetsedwa kwa Farao
1Ndipo Yosefe analowa nauza Farao nati, Atate wanga ndi abale anga, ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao, ndi zonse ali nazo, anachokera ku dziko la Kanani; ndipo, taonani, ali m'dziko la Goseni. 2Ndipo mwa abale ake anatengako anthu asanu, nawaonetsa iwo kwa Farao. 3Ndipo Farao anati kwa abale ake, Ntchito yanu njotani? Ndipo iwo anati kwa Farao, Akapolo anu ndi abusa, ife ndi atate athu. 4#Gen. 15.13; Deut. 26.5Nati kwa Farao, Tafika kuti tikhale m'dzikomo; popeza palibe podyetsa zoweta za akapolo anu; pakuti njala yakula m'dziko la Kanani. Mulole tsopano akapolo anu akhale m'dziko la Goseni. 5Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Atate wako ndi abale ako afika kwa iwe; 6#Eks. 18.21dziko la Ejipito lili pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m'dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang'anire ng'ombe zanga. 7Ndipo Yosefe analowa naye Yakobo atate wake, namuika iye pamaso pa Farao; ndipo Yakobo anamdalitsa Farao. 8Ndipo Farao anati kwa Yakobo, Masiku a zaka za moyo wanu ndi angati? 9#1Mbi. 29.15; Mas. 39.12; Aheb. 11.9Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao. 10Ndipo Yakobo anamdalitsa Farao, natuluka pamaso pa Farao. 11Ndipo Yosefe anakhazika atate wake ndi abale ake, napatsa iwo pokhala m'dziko la Ejipito, m'dera lokometsetsa la m'dziko, m'dziko la Ramsesi, monga analamulira Farao. 12Ndipo Yosefe anachereza atate wake ndi abale ake, ndi mbumba yonse ya atate wake ndi chakudya monga mwa mabanja ao.
Yosefe agulira Farao dziko la Ejipito
13Ndipo munalibe chakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chake dziko la Ejipito ndi dziko la Kanani linalefuka chifukwa cha njalayo. 14Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama kunyumba ya Farao. 15Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, Aejipito onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife chakudya; tiferenji pamaso panu? Zatsirizika ndalama. 16Ndipo Yosefe anati, Mundipatse ng'ombe zanu: ndipo ndidzakupatsani inu mtengo wa ng'ombe zanu ngati ndalama zatsirizika. 17Ndipo anadza nazo ng'ombe zao kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo chakudya chosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi abulu; ndipo anawadyetsa iwo ndi chakudya chosinthana ndi zoweta zao zonse chaka chimenecho. 18Chitatha chaka chimenecho, anadza kwa iye chaka chachiwiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng'ombe nza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu; 19#Neh. 5.2-3tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? Mutigule ife ndi dziko lathu ndi chakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja. 20Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Ejipito, chifukwa Aejipito anagulitsa yense munda wake, chifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao. 21Tsono anthu, anasunthira iwo kumizinda kuchokera kumphepete kwa malire a Ejipito kufikira kumphepete kwina kwake. 22#Ezr. 7.24Koma dziko la ansembe lokha sanagule, chifukwa ansembe analandira gawo lao kwa Farao, nadya gawolo anawapatsa Farao; chifukwa chake sanagulitse dziko lao. 23Ndipo Yosefe anati kwa anthu, Taonani, ndamgulira Farao inu ndi dziko lanu lero lomwe, taonani, mbeu zanu siizi, mubzale m'dziko. 24#Gen. 41.34Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za chakudya chanu, ndi cha ana anu ndi mabanja anu. 25Ndipo iwo anati, Watipulumutsa miyoyo yathu; tipeze ufulu pamaso pa mbuyanga, ndipo tidzakhala akapolo a Farao. 26#Gen. 47.22Ndipo Yosefe analamulira lamulo la padziko la Ejipito kufikira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhale la Farao. 27Ndipo Israele anakhala m'dziko la Ejipito, m'dziko la Goseni; nakhala nazo zaozao m'menemo, nabalana nachuluka kwambiri.
28 #
Gen. 47.9
Ndipo Yakobo anakhala m'dziko la Ejipito zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri; ndipo masiku a Yakobo zaka za moyo wake zinali zaka zana limodzi mphambu makumi anai kudza zisanu ndi ziwiri. 29#Gen. 24.2; 50.25Ndipo nthawi inayandikira kuti Israele adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga, nundichitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine mu Ejipito; 30#Gen. 49.29koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m'dziko la Ejipito, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena. 31#Gen. 48.2; 1Maf. 1.47; Aheb. 11.21Ndipo anati, Undilumbirire ine; namlumbirira iye. Ndipo Israele anawerama kumutu kwa kama.
Currently Selected:
GENESIS 47: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi