YouVersion Logo
Search Icon

GENESIS 50

50
Maliro a Yakobo
1Ndipo Yosefe anagwa pa nkhope ya atate wake, namlirira iye nampsompsona iye. 2#2Mbi. 16.14; Yoh. 19.40Ndipo Yosefe anauza akapolo ake asing'anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israele. 3Ndipo anatha masiku ake makumi anai a iye; chifukwa chomwecho amatsiriza masiku akukonza thupi; ndipo Aejipito anamlira iye masiku makumi asanu ndi awiri.
4Atapita masiku akumlira iye, Yosefe anati kwa mbumba ya Farao, kuti, Ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, nenanitu m'makutu a Farao kuti, 5#Gen. 47.29Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Taona, ndilinkufa; m'manda m'mene ndadzikonzeratu ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso. 6Ndipo Farao anati, Pita, kaike atate wako, monga iye anakulumbiritsa iwe. 7Ndipo Yosefe anapita kukaika atate wake; ndipo anakwera pamodzi ndi akapolo onse a Farao, ndi akulu a pa mbumba yake, ndi akulu onse a m'dziko la Ejipito, 8ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ake, ndi mbumba ya atate wake: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni. 9Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magaleta ndi apakavalo; ndipo panali khamu lalikulu. 10Ndipo anafika pa dwale la Atadi, lili tsidya lija la Yordani, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi. 11Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro aakulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani. 12Ndipo ana ake aamuna anamchitira iye monga anawalamulira iwo; 13#Gen. 49.29-30chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure.
14Ndipo ataika atate wake, Yosefe anabwera ku Ejipito, iye ndi abale ake, ndi onse amene anakwera pamodzi naye kukaika atate wake. 15Ndipo pamene abale ake a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamchitira iye. 16Ndipo anatumiza mthenga kwa Yosefe kuti, Atate wathu asanafe analamulira, kuti, 17Muziti chotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kuchimwa kwao, chifukwa kuti anakuchitirani inu choipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa akapolo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye. 18#Gen. 37.7, 10Ndiponso abale ake anamuka namgwadira pamaso pake; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu. 19Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Musaope; pakuti ndili ine kodi m'malo a Mulungu? 20#Gen. 45.5, 9Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri. 21Ndipo tsopano musaope; ine ndidzachereza inu, ndi ana anu aang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.
Kumwalira kwa Yosefe
22Ndipo Yosefe anakhala mu Ejipito, iye, ndi mbumba ya atate wake; ndipo Yosefe anakhala ndi moyo zaka zana limodzi ndi khumi. 23Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe. 24#Gen. 48.21; Eks. 3.16, 17; Aheb. 11.22Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo. 25#Eks. 13.19Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israele kuti, Mulungu adzaonekera kwa inu ndithu, ndipo mudzakwera nao mafupa anga kuchokera kuno. 26#Gen. 50.2Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lake ndi mankhwala osungira, ndipo anamuika iye m'bokosi mu Ejipito.

Currently Selected:

GENESIS 50: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in