MACHITIDWE A ATUMWI 28
28
Paulo pa Melita
1 #
Mac. 27.26
Ndipo titapulumuka, pamenepo tinadziwa kuti chisumbucho chinatchedwa Melita. 2Ndipo akunja anatichitira zokoma zosachitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, chifukwa cha mvula inalinkugwa, ndi chifukwa cha chisanu. 3Koma pamene Paulo adaola chisakata cha nkhuni, nachiika pamoto, inatulukamo njoka, chifukwa cha kutenthaku, niluma dzanja lake. 4Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende pa dzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m'nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo. 5#Luk. 10.19Koma anakutumulira chilombocho kumoto, osamva kupweteka. 6#Mac. 14.11Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wake kugwa kufa pomwepo; koma m'mene adalindira nthawitu, naona kuti sikunampweteka, anapindula, nati, Ndiye Mulungu.
7Koma pafupi pamenepo panali minda, mwini wake ndiye mkulu chisumbucho, dzina lake Publio; amene anatilandira ife, natichereza okoma masiku atatu. 8#Yak. 5.14-15Ndipo kunatero kuti atate wake wa Publioyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namchiritsa. 9Ndipo patachitika ichi, enanso a m'chisumbu, okhala nazo nthenda, anadza, nachiritsidwa; 10amenenso anatichitira ulemu wambiri; ndipo pochoka ife anatiikira zotisowa.
Paulo afika ku Roma, nakhala wandende m'nyumba ya iye yekha zaka ziwiri
11Ndipo itapita miyezi itatu tinayenda m'ngalawa ya ku Aleksandriya, idagonera nyengo ya chisanu kuchisumbuko, chizindikiro chake, Ana Amapasa. 12Ndipo pamene tinakocheza ku Sirakusa, tinatsotsako masiku atatu. 13Ndipo pochokapo tinapaza ntifika ku Regio; ndipo litapita tsiku limodzi unayamba mwera, ndipo m'mawa mwake tinafika ku Puteoli: 14pamenepo tinakomana ndi abale, amene anatiumirira tikhale nao masiku asanu ndi awiri; ndipo potero tinafika ku Roma. 15Kuchokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apio, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.
16 #
Mac. 27.3
Ndipo pamene tinalowa m'Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikali womdikira iye.
17 #
Mac. 21.33; 24.12-13 Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinachita kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam'nsinga kuchokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma; 18#Mac. 25.8; 26.31ndiwo, atandifunsafunsa ine anafuna kundimasula, popeza panalibe chifukwa cha kundiphera. 19#Mac. 25.11Koma pakukanapo Ayuda, ndinafulumidwa mtima kutulukira kwa Kaisara; si kunena kuti ndinali nako kanthu kakunenera mtundu wanga. 20#Mac. 26.6-7Chifukwa cha ichi tsono ndinakupemphani inu mundione ndi kulankhula nane; pakuti chifukwa cha chiyembekezo cha Israele ndamangidwa ndi unyolo uwu. 21Ndipo anati kwa iye, Ife sitinalandira akalata onena za inu ochokera ku Yudeya, kapena sanadza kuno wina wa abale ndi kutiuza kapena kulankhula kanthu koipa ka inu. 22#Luk. 2.34; Mac. 24.5, 14Koma tifuna kumva mutiuze muganiza chiyani; pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponseponse. 23#Luk. 24.27; Mac. 17.3Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo. 24#Mac. 14.4Ndipo ena anamvera zonenedwazo, koma ena sanamvere. 25Koma popeza sanavomerezana, anachoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu, 26#Yes. 6.9-10; Mat. 13.14-15ndi kuti,
Pita kwa anthu awa, nuti,
Ndi kumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse;
ndipo pakupenya mudzapenya, koma osaona konse;
27pakuti mtima wa anthu awa watupatu,
ndipo m'makutu mwao mmolema kumva,
ndipo maso ao anawatseka;
kuti angaone ndi maso,
nangamve ndi makutu,
nangazindikire ndi mtima,
nangatembenuke,
ndipo Ine ndingawachiritse.
28 #
Mat. 21.41, 43; Mac. 13.46-47 Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzamva.#28.28 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 29 Ndipo pamene Paulo adanena mau awa, Ayuda aja adachokapo akutsutsana kwambiri pakati pao.
30Ndipo anakhala zaka ziwiri zamphumphu m'nyumba yake yobwereka, nalandira onse akufika kwa iye, 31#Aro. 11.8; Aef. 6.19ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu.
Currently Selected:
MACHITIDWE A ATUMWI 28: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi