EKSODO Mau Oyamba
Mau Oyamba
Dzina lakuti Eksodo limatanthauza “kutuluka”, ndipo limafotokoza za chinthu chofunikira kwambiri mu mbiri ya Aisraele. Chinthu chimenechi ndicho kusamuka kwa Aisraele kuchokera ku Ejipito kumene anali akapolo. Bukuli lili ndi magawo anai: Gawo loyamba ndilo kumasuka kwa Aisraele ku ukapolo; lachiwiri ndilo ulendo wao kupita kuphiri la Sinai; lachitatu ndi chipangano cha Mulungu ndi anthu ake pa phiri la Sinai, pamene anawapatsa malamulo okhudzana ndi chikhalidwe, kayendetse ka dziko komanso chipembedzo; ndipo gawo lachinai ndilo mamangidwe ndi makonzedwe a malo opembedzerapo Aisraele, ndiponso malamulo okhudzana ndi ansembe komanso chipembedzo.
Kwenikweni bukuli likulongosola zimene Mulungu anachita pamene anawamasula anthu ake ku ukapolo ndi kuwasandutsa kukhala mtundu wa anthu okhala ndi chiyembekezo cha tsogolo labwino.
Mwininkhani mu bukuli ndiye Mose, amene Mulungu anamusankha kuti atsogolere anthu ake kuchokera ku Ejipito. Gawo lodziwika bwino la bukuli ndilo Malamulo Khumi (20.1-17).
Za mkatimu
Aisraele apulumuka ku ukapolo wa ku Ejipito 1.1—15.21
a. Akapolo ku Ejipito 1.1-22
b. Kubadwa kwa Mose ndi ubwana wake 2.1—4.31
c. Mose ndi Aroni akumana ndi mfumu ya Ejipito 5.1—11.10
d. Aisraele achita Paska nachoka ku Ejipito 12.1—15.21
Kuchokera ku Nyanja Yofiira mpaka kuphiri la Sinai 15.22—18.27
Kuperekedwa kwa Malamulo ndi chipangano 19.1—24.18
Malo Opatulika ndi malangizo a chipembedzo 25.1—40.38
Currently Selected:
EKSODO Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi