GENESIS 17
17
Dzina la Abramu lisinthika likhale Abrahamu
1 #
Gen. 6.9; 24.40; 28.3; Deut. 18.13 Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro. 2#Gen. 12.2; 15.18Ndipo ndidzapangana pangano langa ndi Ine ndi iwe, ndipo ndidzachulukitsa iwe kwambiri. 3Ndipo Abramu anagwa nkhope pansi, ndipo Yehova ananena naye kuti, 4#Aro. 4.17Koma Ine, taona, pangano langa lili ndi iwe, ndipo udzakhala iwe atate wa khamu la mitundu. 5#Neh. 9.7Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu. 6#Gen. 17.16Ndipo ndikubalitsa iwe ndithu, ndipo ndidzakuyesa iwe mitundu, ndipo mafumu adzatuluka mwa iwe. 7#Agal. 3.17Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako. 8#Eks. 6.7; Deut. 14.2; Mas. 105.11Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.
Mulungu aika chizindikiro cha kudulidwa
9Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma iwe, uzikumbukira pangano langa, iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao. 10Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu. 11#Aro. 4.11Muzidula khungu lanu; ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano pakati pa Ine ndi inu. 12#Lev. 12.3; Luk. 2.21A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana amuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako. 13Azidulidwatu amene abadwa m'nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m'thupi mwako pangano losatha. 14Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.
Dzina la Sarai lisinthika likhale Sara
15Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usam'tcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara. 16Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amake amitundu, mafumu a anthu adzatuluka mwa iye. 17Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala? 18Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, Ha! Ismaele akhale ndi moyo pamaso panu! 19#Gen. 18.10; 21.2Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake. 20#Gen. 16.10Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu. 21#Gen. 26.2-5Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe yino chaka chamawa. 22Ndipo analeka kunena naye, ndipo Mulungu anakwera kuchokera kwa Abrahamu. 23Ndipo Abrahamu anatenga Ismaele mwana wake ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye. 24Ndipo Abrahamu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, pamene anadulidwa m'khungu lake. 25Ndipo Ismaele mwana wake anali wa zaka khumi ndi zitatu pamene anadulidwa m'khungu lake. 26Tsiku lomwelo anadulidwa Abrahamu ndi Ismaele mwana wake. 27Ndipo amuna onse a m'nyumba mwake obadwa m'nyumba, ndi ogulidwa ndi ndalama kwa alendo, anadulidwa pamodzi naye.
Currently Selected:
GENESIS 17: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi