YouVersion Logo
Search Icon

GENESIS 28

28
1Ndipo Isaki anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani. 2#Hos. 12.12Tauka, nupite ku Padanaramu, kunyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana akazi a Labani mlongo wake wa amai ako. 3Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu: 4akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu. 5Ndipo Isaki anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wake wa Betuele Mwaramu, mlongo wake wa Rebeka, amai wao wa Yakobo ndi Esau.
Yakobo apita ku Padanaramu
6Ndipo anaona Esau kuti Isaki anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko; ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani; 7ndiponso kuti Yakobo anamvera atate wake ndi amake, nanka ku Padanaramu; 8ndipo Esau anaona kuti ana akazi a Kanani sanakondweretsa Isaki atate wake: 9ndipo Esau ananka kwa Ismaele, naonjezera kwa akazi amene anali nao, natenga Mahalati mwana wamkazi wa Ismaele mwana wa Abrahamu, mlongo wake wa Nebayoti akhale mkazi wake.
Loto la Yakobo ku Betele
10Ndipo Yakobo anachoka m'Beereseba, nanka ku Harani. 11Ndipo anafika kumalo, nagona kumeneko usiku, chifukwa lidalowa dzuwa: ndipo anatenga mwala wa kumeneko, nauika pansi pa mutu wake, nagona tulo kumeneko. 12#Num. 12.6; Yoh. 1.51Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo. 13#Gen. 26.24Taonani, Yehova anaima pamwamba pake, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isaki; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako; 14mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa. 15#1Maf. 8.57Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe. 16#Eks. 3.5Ndipo Yakobo anauka m'tulo take, nati, Ndithu, Yehova ali mommuno; ndipo sindinadziwe. 17Ndipo anaopa, nati, Poopsa pompano! Pompano ndipo pa nyumba ya Mulungu, si penai, pompano ndipo pa chipata cha kumwamba. 18#1Sam. 7.12Yakobo ndipo anauka m'mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pa mutu wake, nauimiritsa, nathira mafuta pamtu pake. 19Ndipo anatcha dzina la pamenepo Betele; pakuyamba dzina lake la mudziwo ndi Luzi. 20#Gen. 31.13Yakobo ndipo analumbira chilumbiro, nati, Mulungu akakhala ndi ine, akandisunga ine m'njira imene ndipitamo, akandipatsa ine mkate wa kudya, ndi zovalira za kuvala, 21#Deut. 26.17; Ower. 11.31kuti ndibwerenso kunyumba ya atate wanga ndi mtendere, pamenepo Yehova adzakhala Mulungu wanga, 22#Gen. 14.20ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi.

Currently Selected:

GENESIS 28: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in