GENESIS 33
33
Yakobo ayanjanitsidwa ndi Esau
1Ndipo Yakobo anatukula maso ake, taonani, anadza Esau, ndi pamodzi naye anthu mazana anai. Ndipo anagawira ana kwa Leya, ndi kwa Rakele, ndi kwa adzakazi awiri aja. 2Ndipo anaika adzakazi ndi ana ao patsogolo, ndi Leya ndi ana ake pambuyo pao, ndi Rakele ndi Yosefe pambuyo pa onse. 3Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pao, nawerama pansi kasanu ndi kawiri mpaka anayandikira mkulu wake. 4Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo. 5#Mas. 127.3; Yes. 8.18Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu. 6Ndipo adzakazi anayandikira ndi ana ao, nawerama pansi. 7Ndiponso Leya ndi ana ake anayandikira nawerama pansi: pambuyo pake anayandikira Yosefe ndi Rakele, nawerama pansi. 8Ndipo anati, Nanga khamu lonse limene ndinakomana nalo nlotani? Ndipo anati, Kuti ndipeze ufulu pamaso pa mbuyanga. 9Ndipo Esau anati, Zanga zindifikira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha. 10Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga pa dzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine. 11Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindifikira. Ndipo anamkakamiza, nalandira. 12Ndipo Esau anati, Tiyeni timuke; nditsogolera ndine. 13Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali ambowa, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa. 14Mbuyanga atsogoleretu kapolo wake, ndipo ine ndidzazitsogolera pang'onopang'ono monga mwa mayendedwe a zoweta zili pamaso panga, ndi monga mwa mayendedwe a ana, mpaka ndifike kwa mbuyanga ku Seiri. 15Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? Ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga. 16Ndipo Esau anabwera tsiku lomwelo kunka ku Seiri. 17Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namanga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti.
Yakobo afika ku Sekemu
18Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumudzi wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mudzipo. 19#Yos. 24.32Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga hema wake, pa dzanja la ana ake a Hamori atate wake wa Sekemu. 20Ndipo anamanga pamenepo guwa la nsembe, natcha pamenepo El-Elohe-Israele.
Currently Selected:
GENESIS 33: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi