GENESIS 44
44
Abalewo ayesedwa ndi Yosefe
1Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wake kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi chakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lake. 2Nuike chikho changa, chikho chasiliva chija, kukamwa kwa thumba la wamng'ono, pamodzi ndi ndalama za tirigu zake. Ndipo iye anachita monga mau ananena Yosefe. 3Pamene kudacha, anamukitsa anthu iwo ndi abulu ao. 4Atatuluka m'mudzi asanamuke patali, Yosefe anati kwa tsanyumba wake, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Chifukwa chanji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino? 5Kodi si ndicho chomwera nacho mbuyanga, naombeza ula nacho? Mwachitira choipa pakutero. 6Ndipo anapeza iwo, nanena nao mau omwewo. 7Nati kwa iye, Bwanji mbuyanga anena mau otere? Ngati nkutheka kuti akapolo anu achite chotero? 8Taonani, ndalama zija, tinazipeza kukamwa kwa matumba athu, tinazibwezanso kwa inu kutuluka m'dziko la Kanani; nanga bwanji tingabe m'nyumba ya mbuyanga kapena siliva kapena golide? 9#Gen. 31.32Iye wa akapolo anu ampeza nacho afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga. 10Ndipo iye anati, Tsononso chikhale monga mwa mau anu: iye amene ampeza nacho adzakhala kapolo wanga; ndipo inu mudzakhala opanda chifukwa. 11Ndipo anafulumira natsitsa pansi yense thumba lake, namasula yense thumba lake. 12Ndipo iye anafunafuna kuyambira pa wamkulu naleka pa wamng'ono nachipeza chikho m'thumba la Benjamini: 13#Gen. 37.29ndipo anang'amba zovala zao, nasenzetsa yense bulu wake, nabwera kumudzi. 14#Gen. 37.7, 9-10; 42.6Yudanso ndi abale ake anadza kunyumba ya Yosefe; ndipo iye akali pamenepo; ndipo anagwa pansi patsogolo pake. 15Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ichi nchiyani mwachichita? Kodi simudziwa kuti munthu ngati ine ndingathe kuzindikira ndithu?
Yuda apembedzera Benjamini kwa Yosefe
16Ndipo Yuda anati, Kodi tidzati bwanji kwa mbuyanga? Kodi tidzanenanji? Kapena tidzawiringula ife bwanji? Mulungu wapeza mphulupulu ya akapolo anu; taonani, tili akapolo a mbuyanga, ife ndi iye amene anampeza nacho chikho m'dzanja lake. 17Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndichite chotero! Munthu amene anampeza nacho m'dzanja lake adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu.
18Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao. 19Mbuyanga anafunsa akapolo ake kuti, Kodi muli ndi atate wanu kapena mbale wanu? 20Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng'ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye. 21#Gen. 42.15Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m'maso mwanga. 22Ndipo ife tinati kwa mbuyanga, Mnyamata sangathei kumsiya atate wake; pakuti akamsiya atate wake, atate wake adzafa. 23#Gen. 43.3Ndipo munati kwa akapolo anu, Koma ngati mbale wanu safika pamodzi ndi inu, simudzaonanso konse nkhope yanga. 24Ndipo panali titakwera kunka kwa kapolo wanu atate wanga, tinamfotokozera iye mau a mbuyanga. 25Ndipo atate wathu anati, Mupitenso mutigulire ife chakudya pang'ono. 26Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng'ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingaone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng'ono akapanda kukhala ndi ife. 27Ndipo kapolo wanu atate wanga anati kwa ife, Inu mudziwa kuti mkazi wanga anandibalira ine ana amuna awiri; 28#Gen. 37.33wina anatuluka kwa ine ndipo ndinati, Zoonatu, wakadzulidwa; ndipo sindidzamuonanso iye; 29#Gen. 42.38ndipo ngati mukandichotsera ameneyonso, ndipo ngati chimgwera choipa, mudzanditsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda. 30Chifukwa chake ndikafika kwa kapolo wanu atate wanga, ndipo mnyamata akapanda kukhala ndi ife; popeza moyo wanu uli womangidwa ndi moyo wa mnyamatayo; 31kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi chisoni imvi za atate wathu kumanda. 32Pakuti kapolo wanu anadziyesa chikole cha mnyamata pa atate wanga, kuti, Ndikapanda kumbwezeranso kwa inu, pamenepo ndidzakhala ndi chifukwa kwa atate wanga nthawi zonse. 33Tsopanotu, mtumiki wanu akhale kapolo wa mbuyanga m'malo mwa mnyamata; mnyamatayo akwere pamodzi ndi abale ake. 34Pakuti ndidzakwera bwanji kwa atate wanga, mnyamatayo akapanda kukhala ndi ine? Ndingaone choipa chidzagwera atate wanga.
Currently Selected:
GENESIS 44: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi