GENESIS 46
46
Yakobo atsikira ku Ejipito
1Ndipo Israele anamuka ulendo wake ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isaki atate wake. 2Ndipo Mulungu ananena kwa Israele, m'masomphenya a usiku, nati, Yakobo, Yakobo. 3#Gen. 26.24; 35.11Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Ejipito; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu; 4#Num. 20.15-16Ine ndidzatsikira pamodzi ndi iwe ku Ejipito; ndipo Ine ndidzakubwezanso ndithu; ndipo Yosefe adzaika dzanja lake pamaso pako. 5Ndipo Yakobo anachoka ku Beereseba, ndipo ana amuna a Israele anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao ang'ono, ndi akazi ao, m'magaleta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye. 6#Yos. 24.4Ndipo anatenga ng'ombe zao ndi chuma chao anachipeza m'dziko la Kanani, nadza ku Ejipito, Yakobo ndi mbeu zake zonse pamodzi ndi iye; 7ana ake amuna, ndi zidzukulu zake zazimuna, ndi ana akazi ake, ndi zidzukulu zake zazikazi, ndi mbeu zake zonse anadza nazo m'Ejipito.
8Maina a ana a Israele amene anadza m'Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana amuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo. 9Ndi ana amuna a Rubeni: Hanoki, ndi Palu, ndi Hezironi, ndi Karimi. 10Ndi ana amuna a Simeoni: Yemuwele ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani. 11Ndi ana amuna a Levi: Geresoni, Kohati, ndi Merari. 12Ndi ana amuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana amuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli. 13Ndi ana amuna a Isakara: Tola ndi Puva, ndi Iyobu, ndi Simironi. 14Ndi ana amuna a Zebuloni: Seredi, ndi Eloni ndi Yaleele. 15Amenewo ndi ana amuna a Leya, amene anambalira Yakobo m'Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wake Dina; ana aamuna ndi aakazi onse ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu. 16Ndi ana amuna a Gadi: Zifiyoni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Eziboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli. 17Ndi ana amuna a Asere: Imina, ndi Isiva, ndi Isivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikiele. 18Amenewa ndi ana a Zilipa, amene Labani anampatsa Leya mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo, anthu khumi ndi asanu ndi mmodzi. 19Ana a Rakele mkazi wake wa Yakobo: Yosefe ndi Benjamini. 20Kwa Yosefe kunabadwa m'dziko la Ejipito Manase ndi Efuremu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye. 21Ndi ana amuna a Benjamini: Bela ndi Bekere, ndi Asibele, ndi Gera, ndi Naamani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi. 22Amenewo ndi ana a Rakele, amene anabadwira Yakobo; anthu onse ndiwo khumi ndi anai. 23Ndi ana amuna a Dani: Husimu. 24Ndi ana amuna a Nafutali: Yazeele, ndi Guni, ndi Yezere ndi Silemu 25Amenewa ndi ana a Biliha, amene Labani anampatsa Rakele mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo asanu ndi awiri. 26#Eks. 1.5Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo m'Ejipito, amene anatuluka m'chuuno mwake, pamodzi ndi akazi a ana amuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi; 27ndi ana amuna a Yosefe, amene anambadwira iye m'Ejipito ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa m'Ejipito anali makumi asanu ndi awiri.
Yakobo akomana ndi Yosefe
28Ndipo anatumiza Yuda patsogolo pake kwa Yosefe, amtsogolere kumuonetsa njira yonka ku Goseni: ndipo anafika ku dziko la Goseni. 29Ndipo Yosefe anamanga galeta lake nakwera kunka kukakomana naye Israele atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m'kulira pakhosi pake. 30#Luk. 2.29-30Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Ndife tsopano, popeza ndaona nkhope yako, kuti ukali ndi moyo. 31Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, ndi kwa mbumba ya atate wake, Ndidzanka, ndikauze Farao, ndipo ndidzati kwa iye, Abale anga ndi mbumba ya atate wanga, amene anali m'dziko la Kanani, afika kwa ine; 32ndipo anthuwo ali abusa chifukwa anakhala oweta ng'ombe; ndipo anadza ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao ndi zonse ali nazo. 33Ndipo padzakhala pamene Farao adzaitana inu, nadzati, Ntchito yanu njotani? 34#Gen. 43.32; Eks. 8.26Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito.
Currently Selected:
GENESIS 46: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi