GENESIS 48
48
Yakobo adalitsa ana a Yosefe
1Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake amuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye. 2Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Israele anadzilimbitsa nakhala tsonga pakama. 3#Gen. 17.1Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine, 4#Gen. 28.3Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakuchulukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao chikhalire. 5#Yos. 13.7; 14.4Tsopano ana ako amuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga. 6Koma obala iwe udzawabala pambuyo pao, ndiwo ako; awatche dzina la abale ao m'cholowa chao. 7#Gen. 35.19Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efurata; ndipo ndidamuika iye pamenepo pa njira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu). 8Ndipo Israele anayang'ana ana amuna a Yosefe, nati, Ndani awa? 9#Aheb. 11.21Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa. 10Koma maso a Israele anali akhungu m'ukalamba wake, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira. 11Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndione nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe. 12Ndipo Yosefe anatulutsa iwo pakati pa maondo ake, nawerama ndi nkhope yake pansi. 13Ndipo Yosefe anatenga iwo onse awiri, Efuremu m'dzanja lake lamanja ku dzanja lamanzere la Yakobo, ndi Manase m'dzanja lake lamanzere ku dzanja lamanja la Israele, nadza nao pafupi ndi iye. 14Ndipo Israele anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pa mutu wa Efuremu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lake lamanzere pa mutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba. 15Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pake anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isaki, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero, 16#Eks. 23.20; Amo. 9.12; Mac. 15.17mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati pa dziko lapansi. 17Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wake anaika dzanja lake lamanja pa mutu wa Efuremu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wake, kulichotsa pa mutu wa Efuremu ndi kuliika pa mutu wa Manase. 18Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pa mutu wake. 19Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri. 20Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israele adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efuremu ndi monga Manase; ndipo anaika Efuremu woyamba wa Manase. 21#Gen. 50.24Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako. 22#Yos. 24.32Ndipo ine ndakupatsa iwe gawo limodzi loposa la abale ako, limene ndinalanda m'dzanja la Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.
Currently Selected:
GENESIS 48: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi