LUKA 12
12
Yesu awachenjeza za chinyengo
(Mat. 16.5-12)
1 #
Mat. 16.12
Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo. 2#Mat. 10.26Koma kulibe kanthu kovundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika. 3Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwalankhula m'khutu, m'zipinda za m'kati chidzalalikidwa pa machindwi a nyumba.
Awatchulira amene ayenera kumuopa
(Mat. 10.29-33)
4 #
Yer. 1.8
Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musaope iwo akupha thupi, ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angathe kuchita. 5Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya ku Gehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.
6Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu; 7komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri. 8#Mat. 10.32; Mrk. 8.38; 2Tim. 2.12; 1Yoh. 2.23Ndipo ndinena kwa inu, Amene aliyense akavomereza Ine pamaso pa anthu, inde, Mwana wa Munthu adzamvomereza iye pamaso pa angelo a Mulungu; 9#Mat. 10.32; Mrk. 8.38; 2Tim. 2.12; 1Yoh. 2.23Koma iye wondikana Ine pamaso pa anthu, iye adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu. 10#Mat. 12.31-32; 1Yoh. 5.16Ndipo amene aliyense adzanenera Mwana wa Munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa. 11#Mat. 10.19Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani; 12pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena.
Fanizo la mwini chuma wopusa
13Ndipo munthu wa m'khamulo anati kwa Iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine chuma chamasiye. 14#Yoh. 18.36Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu? 15#1Tim. 6.7-9Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo. 16Ndipo Iye ananena nao fanizo, kuti, Munda wake wa munthu mwini chuma unapatsa bwino. 17Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndilibe mosungiramo zipatso zanga? 18Ndipo anati Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi chuma changa. 19#Mlal. 11.9; 1Ako. 15.32Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere. 20#Mas. 52.7Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani? 21#Mat. 6.20Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.
Nkhawa za moyo wathu
(Mat. 6.25-34)
22Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala. 23Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. 24#Mas. 147.9Lingirirani makungubwi, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri! 25Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wake? 26Kotero ngati simungathe ngakhale chaching'onong'ono, muderanji nkhawa chifukwa cha zina zija? 27#1Maf. 10.4-7Lingalirani maluwa, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomoni, mu ulemerero wake wonse sanavale ngati limodzi la awa. 28Koma ngati Mulungu aveka kotere udzu wa kuthengo ukhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang'ono? 29Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya, ndi chimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima. 30Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi. 31#Mat. 6.33Komatu tafunafunani Ufumu wake, ndipo izi adzakuonjezerani. 32#Mat. 11.25-26Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu. 33#Mat. 6.20; 19.21; 1Tim. 6.19Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga. 34Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.
Fanizo la kapolo wochezera
(Mat. 24.42-51)
35 #
Mat. 25.1-13; Aef. 6.14 Khalani odzimangira m'chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka; 36ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kuchokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo. 37#Mat. 24.45-46Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira. 38Ndipo akadza ulonda wachiwiri, kapena wachitatu, nakawapeza atero, odala amenewa.
39 #
Mat. 24.43
Koma zindikirani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yake yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yake ibooledwe. 40#Mat. 24.43Khalani okonzeka inunso; chifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa Munthu akudza. 41Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse? 42Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kapitao wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yake? 43#Mat. 24.46Wodala kapoloyo amene mbuye wake pakufika, adzampeza alikuchita chotero. 44Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo. 45#Mat. 24.48-49Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera; 46#Mat. 24.50-51mbuye wa kapolo uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati nadzamuika dera lake pamodzi ndi anthu osakhulupirira. 47#Yoh. 9.41; Yoh. 15.22; Mac. 17.30Ndipo kapolo uyo, wodziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sanakonza, ndi kusachita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri. 48#1Tim. 1.13Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.
Yesu aponya moto pa dziko lapansi
(Mat. 10.34-36)
49Ine ndinadzera kuponya moto pa dziko lapansi; ndipo ndifunanji ngati unatha kuyatsidwa? 50Koma ndili ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa! 51Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere pa dziko lapansi? Ndinena kwa inu, Iaitu, komatu kutsutsana; 52#Mat. 10.34-35pakuti kuyambira tsopano adzakhala m'nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu. 53Adzatsutsana atate ndi mwana wake, ndi mwana ndi atate wake; amake adzatsutsana ndi mwana wamkazi, ndi mwana wamkazi ndi amake, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndi mkaziyo ndi mpongozi wake.
Zizindikiro za nyengo yake
54 #
Mat. 16.2-3
Koma Iye ananenanso kwa makamu a anthu, Pamene paliponse muona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti, Ikudza mvula; ndipo itero. 55Ndipo pamene mphepo ya kumwera iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi. 56Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo yino? 57Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama? 58#Miy. 25.8; Mat. 5.25Pakuti pamene ulikupita naye mnzako wa mlandu kwa oweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa oweruza, ndipo oweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, ndi msilikali angaponye iwe m'nyumba yandende. 59#Mat. 5.26Ine ndinena kwa iwe, Sudzatulukamo konse kufikira utalipira kakobiri kukumaliza.
Currently Selected:
LUKA 12: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi