LUKA 23
23
Yesu pa bwalo la Pilato
(Mat. 26.57-68; Mrk. 14.53-65; Yoh. 18.12-27)
1Ndipo khamu lonselo linanyamuka kupita naye kwa Pilato. 2#Mat. 17.27; 22.21; Yoh. 19.12; Mac. 17.7Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu. 3Ndipo Pilato anamfunsa Iye, nanena, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Iye anamyankha nati, Mwatero. 4Ndipo Pilato anati kwa ansembe aakulu ndi makamu a anthu, Ndilibe kupeza chifukwa cha mlandu ndi munthu uyu. 5Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa m'Yudeya lonse, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe. 6Koma pamene Pilato anamva, anafunsa ngati munthuyu ali Mgalileya. 7#Luk. 3.1Ndipo m'mene anadziwa kuti ali wa m'ulamuliro wake wa Herode, anamtumiza Iye kwa Herode, amene anali iye mwini ku Yerusalemu masiku awa.
Yesu atumidwa kwa Herode
8 #
Mat. 14.1; Luk. 9.9 Ndipo Herode, pamene anaona Yesu, anakondwa ndithu; pakuti anayamba kale kufuna kumpenya Iye, chifukwa anamva za Iye; nayembekeza kuona chizindikiro china chochitidwa ndi Iye. 9Ndipo anamfunsa Iye mau ambiri; koma Iye sanamyankhe kanthu. 10Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anaimirira, namnenera Iye kolimba. 11#Yes. 53.3Ndipo Herode ndi asilikali ake anampeputsa Iye, namnyoza, namveka Iye chofunda chonyezimira, nambwezera kwa Pilato. 12#Mac. 4.27Ndipo Herode ndi Pilato anachitana chibwenzi tsiku lomwelo; pakuti kale anadana.
Yesu abwezedwa kwa Pilato. Baraba amasulidwa. Yesu amangidwa
(Mat. 27.15-26; Mrk. 15.6-15; Yoh. 18.39-40)
13Ndipo Pilato anaitana ansembe aakulu, ndi akulu, ndi anthu, asonkhane, 14nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeza pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mumnenera; 15inde, ngakhale Herode yemwe; pakuti iye anambwezera Iye kwa ife; ndipo taonani, sanachite Iye kanthu kakuyenera kufa. 16#Yoh. 19.1Chifukwa chake ndidzamkwapula ndi kummasula Iye.#23.16 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 17 Pilato amayenera kuwamasulira wam'ndende mmodzi pa nyengo ya chikondwerero cha Paska. 18#Mac. 3.14Koma iwo onse pamodzi anafuula, nati, Chotsani munthu uyu, mutimasulire Barabasi; 19ndiye munthu anaponyedwa m'ndende chifukwa cha mpanduko m'mudzi ndi cha kupha munthu. 20Ndipo Pilato analankhulanso nao, nafuna kumasula Yesu; 21koma iwo anafuula, nanena, Mpachikeni, mpachikeni pamtanda. 22Ndipo anati kwa iwo nthawi yachitatu, Nanga munthuyu anachita choipa chiyani? Sindinapeza chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamkwapula Iye ndi kummasula. 23Koma anakakamiza ndi mau okweza, napempha kuti Iye apachikidwe. Ndipo mau ao analakika. 24#Mrk. 15.15; Yoh. 19.16Ndipo Pilato anaweruza kuti chimene alikufunsa chichitidwe. 25Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende chifukwa cha mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa chifuniro chao.
Yesu pa njira ya ku Gologota
(Mat. 27.32-33)
26 #
Mat. 27.32; Mrk. 15.21 Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pake pa Yesu.
27Ndipo unamtsata unyinji waukulu wa anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pachifuwa, namlirira Iye. 28Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana akazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu. 29#Mat. 24.19Chifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa. 30#Yes. 2.19Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, Bisani ife. 31#Yer. 25.29Pakuti ngati azichitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma? 32#Yes. 53.12Ndipo analinso awiri ena, ndiwo ochita zoipa, anatengedwa pamodzi ndi Iye kuti aphedwe.
Yesu apachikidwa pamtanda
(Mat. 27.33-56; Mrk. 15.21-41; Yoh. 19.17-37)
33Ndipo pamene anafika kumalo dzina lake Bade, anampachika Iye pamtanda pomwepo, ndi ochita zoipa omwe, mmodzi kudzanja lamanja ndi wina kulamanzere. 34#Mas. 22.18; Mrk. 15.24; Mac. 3.17Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere. 35#Mrk. 15.29Ndipo anthu anaima alikupenya. Ndi akulunso anamlalatira Iye, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake. 36Ndipo asilikalinso anamnyoza, nadza kwa Iye, nampatsa vinyo wosasa, 37nanena, Ngati Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda, udzipulumutse wekha. 38#Mrk. 15.26Ndipo kunalinso lembo pamwamba pake, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YA AYUDA.
39 #
Mrk. 15.32
Ndipo mmodzi wa ochita zoipa anapachikidwawo anamchitira Iye mwano nanena, Kodi suli Khristu Iwe? Udzipulumutse wekha ndi ife. 40Koma winayo anayankha, namdzudzula iye, nati, Kodi suopa Mulungu, poona uli m'kulangika komweku? 41Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tilikulandira zoyenera zimene tinazichita: koma munthu uyu sanachite kanthu kolakwa. 42Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukireni m'mene mulowa Ufumu wanu. 43Ndipo Iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine m'Paradaiso.
44 #
Mrk. 15.33
Ndipo ora lake pamenepo linali ngati lachisanu ndi chimodzi. Ndipo panali mdima pa dziko lonse kufikira ora lachisanu ndi chinai, ndipo dzuwa linada. 45#Mrk. 15.38Ndipo nsalu yotchinga ya m'Kachisi inang'ambika pakati. 46#Mrk. 15.37Ndipo pamene Yesu anafuula ndi mau akulu, anati, Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake. 47#Mrk. 15.39Ndipo pamene kenturiyo anaona chinachitikacho, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama. 48Ndipo makamu onse osonkhana kudzapenya ichi, pamene anaona zinachitikazo, anapita kwao ndi kudziguguda pachifuwa. 49#Mrk. 15.30Ndipo omdziwa Iye onse, ndi akazi amene adamtsata kuchokera ku Galileya, anaima kutali, naona zinthu izi.
Aika maliro a Yesu
(Mat. 27.57-66; Mrk. 15.42-47; Yoh. 19.38-42)
50Ndipo taonani, munthu dzina lake Yosefe, ndiye mkulu wa milandu, munthu wabwino ndi wolungama 51(amene sanavomereze kuweruza kwao ndi ntchito yao) wa ku Arimatea, mudzi wa Ayuda, ndiye woyembekezera Ufumu wa Mulungu, 52yemweyo anapita kwa Pilato napempha mtembo wake wa Yesu. 53#Mrk. 15.46Ndipo anautsitsa, naukulunga m'nsalu yabafuta, nauika m'manda osemedwa m'mwala, m'menemo sanaike munthu ndi kale lonse. 54Ndipo panali tsiku lokonzera, ndi Sabata linayandikira. 55#Mrk. 15.47; Luk. 8.2Ndipo akazi, amene anachokera naye ku Galileya, anatsata m'mbuyo, naona manda, ndi maikidwe a mtembo wake. 56#Eks. 20.10; Mrk. 16.1Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo.
Currently Selected:
LUKA 23: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi