YouVersion Logo
Search Icon

LUKA 4:5-8

LUKA 4:5-8 BLPB2014

Ndipo m'mene anamtsogolera anakwera naye, namuonetsa Iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m'kamphindi kakang'ono. Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wao: chifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna. Chifukwa chake ngati Inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Ambuye Mulungu wako uzimgwadira, ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.