LUKA 4
4
Kuyesedwa kwa Yesu
(Mat. 4.1-11; Mrk. 1.12-13)
1Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordani, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu 2#Eks. 34.28; 1Maf. 19.8kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai. Ndipo Iye sanadye kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala. 3Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mkate. 4#Deut. 8.3Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,
Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha.
5Ndipo m'mene anamtsogolera anakwera naye, namuonetsa Iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m'kamphindi kakang'ono. 6#Yoh. 12.31Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wao: chifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna. 7Chifukwa chake ngati Inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu. 8#Deut. 6.13Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,
Ambuye Mulungu wako uzimgwadira,
ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.
9Ndipo anamtsogolera Iye ku Yerusalemu, namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisiyo, nati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi; 10#Mas. 91.11-12pakuti kwalembedwa kuti,
Adzalamula angelo ake za iwe, kuti akutchinjirize.
11Ndipo,
Pa manja ao adzakunyamula iwe,
kuti ungagunde konse phazi lako pamwala.
12 #
Deut. 6.16
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa,
Usamuyese Ambuye Mulungu wako.
13 #
Aheb. 4.15
Ndipo mdierekezi, m'mene adamaliza mayesero onse, analekana naye kufikira nthawi ina.
Yesu aphunzitsa ku Nazarete nachotsedwako
(Mat. 13.54-58; Mrk. 6.1-6)
14 #
Luk. 4.1
Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira. 15Ndipo Iye anaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalemekezedwa ndi anthu onse.
16Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata. 17Ndipo anapereka kwa Iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo m'mene Iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa,
18 #
Yes. 61.1-2
Mzimu wa Ambuye uli pa Ine,
chifukwa chake Iye anandidzoza Ine
ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino:
anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe,
ndi akhungu kuti apenyanso,
kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,
19kulalikira chaka chosankhika cha Ambuye.
20Ndipo m'mene Iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa Iye. 21Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu. 22#Mas. 45.2; Mrk. 6.2Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe? 23Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno. 24#Mrk. 6.4; Yoh. 4.44Ndipo Iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika kudziko la kwao. 25#1Maf. 17.9Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri m'Israele masiku ake a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikulu pa dziko lonselo; 26ndipo Eliya sanatumidwa kwa mmodzi wa iwo, koma ku Sarepta wa ku Sidoni, kwa mkazi wamasiye. 27#2Maf. 5.1-14Ndipo munali akhate ambiri m'Israele masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe mmodzi wa iwo anakonzedwa, koma Naamani yekha wa ku Siriya. 28Ndipo onse a m'sunagogemo anadzala ndi mkwiyo pakumva izi; 29nanyamuka namtulutsira Iye kunja kwa mudziwo, nanka naye pamutu pa phiri pamene panamangidwa mudzi wao, kuti akamponye Iye pansi. 30#Yoh. 10.39Koma Iye anapyola pakati pao, nachokapo.
Yesu achiritsa munthu wogwidwa ndi chiwanda
(Mrk. 1.23-28)
31Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mudzi wa ku Galileya. Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake; 32#Mat. 7.28-29chifukwa mau ake anali ndi ulamuliro. 33#Mrk. 1.23Ndipo munali m'sunagoge munthu, wokhala nacho chiwanda chonyansa; nafuula ndi mau olimba, kuti, 34#Luk. 4.41Ha! Tili ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi munadza kutiononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu. 35Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m'mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosamphweteka konse. 36Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka. 37Ndipo mbiri yake ya Iye inafalikira kumalo onse a dziko loyandikira.
Yesu achiritsa mpongozi wa Simoni
(Mat. 8.14-17; Mrk. 1.29-34)
38Ndipo Iye ananyamuka kuchokera m'sunagoge, nalowa m'nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wake wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye. 39Ndipo Iye anaimirira, naweramira pa iye, nadzudzula nthendayo; ndipo inamleka iye: ndipo anauka msangatu, nawatumikira.
40 #
Mrk. 1.32
Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene anali nao odwala ndi nthenda za mitundumitundu, anadza nao kwa Iye; ndipo Iye anaika manja ake pa munthu aliyense wa iwo, nawachiritsa. 41Ndi ziwanda zomwe zinatuluka mwa ambiri, ndi kufuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo Iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, chifukwa zinamdziwa kuti Iye ndiye Khristu.
42 #
Mrk. 1.34-35
Ndipo kutacha anatuluka Iye nanka kumalo achipululu; ndi makamu a anthu analikumfunafuna Iye, nadza nafika kwa Iye, nayesa kumletsa Iye, kuti asawachokere. 43Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumidzi yinanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero.
44 #
Mrk. 1.39
Ndipo Iye analikulalikira m'masunagoge a ku Yudeya.
Currently Selected:
LUKA 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi