LUKA 3
3
Kulalikira kwa Yohane Mbatizi
(Mat. 3.1-12; Mrk. 1.2-8; Yoh. 1.6-8, 19-36)
1Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene; 2#Yoh. 11.49; Mac. 4.6pa ukulu wansembe wao wa Anasi ndi Kayafa, panadza mau a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zekariya m'chipululu. 3#Luk. 1.77Ndipo iye anadza kudziko lonse la m'mbali mwa Yordani, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo; 4#Yes. 40.3-5monga mwalembedwa m'buku la Yesaya mneneri, kuti,
Mau a wofuula m'chipululu,
konzani khwalala la Ambuye,
lungamitsani njira zake.
5Chigwa chilichonse chidzadzazidwa,
ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzachepsedwa;
ndipo zokhota zidzakhala zolungama,
ndipo njira za zigoloondo zidzakhala zosalala;
6 #
Yes. 52.10
ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.
7Chifukwa chake iye ananena kwa makamuwo a anthu amene anatulukira kukabatizidwa ndi iye, Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza? 8Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana. 9#Mat. 7.19Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; chotero mtengo uliwonse wosabala chipatso chabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto. 10Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizichita chiyani? 11#2Ako. 8.14Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho. 12#Mat. 21.32Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizichita chiyani? 13#Luk. 19.8Koma iye anati kwa iwo, Musakapambe kanthu konse kakuposa chimene anakulamulirani. 14#Eks. 23.1Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.
15Ndipo pamene anthu anali kuyembekezera, ndipo onse anaganizaganiza m'mitima yao za Yohane, ngati kapena iye ali Khristu; 16Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto: 17#Mat. 13.30amene chouluzira chake chili m'dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake, ndi kusonkhanitsa tirigu m'nkhokwe yake; koma mankhusu adzatentha m'moto wosazima.
18Choteretu iye anauza anthu Uthenga Wabwino ndi kuwadandaulira zinthu zina zambiri. 19#Mat. 14.3Koma Herode mfumu ija, m'mene Yohane anamdzudzula chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndi cha zinthu zonse zoipa Herode anazichita, 20#Mat. 14.3anaonjeza pa zonsezi ichinso, kuti anatsekera Yohane m'nyumba yandende.
Yesu abatizidwa
(Mat. 3.13-17; Mrk. 1.9; Yoh. 1.32-34)
21Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka, 22ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo munatuluka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.
Makolo a Yesu
(Mat. 1.1-17)
23 #
Num. 4.3, 35, 39, 43, 47; Mat. 13.55; Yoh. 6.42 Ndipo Yesuyo, pamene anayamba ntchito yake, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana wa Eli, 24mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Meliki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe, 25mwana wa Matatiasi, mwana wa Amosi, mwana wa Nahumu, mwana wa Hesili, mwana wa Nagai, 26mwana wa Mahati, mwana wa Matatiasi, mwana wa Semeini, mwana wa Yoseke, mwana wa Yoda, 27mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabele, mwana wa Sealatiele, mwana wa Neri, 28mwana wa Meliki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elimadama, mwana wa Eri, 29mwana wa Yose, mwana wa Eliyezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi, 30mwana wa Simeoni, mwana wa Yudasi, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu, 31#2Sam. 5.14; Zek. 12.12mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natamu, mwana wa Davide, 32#Rut. 4.18-22mwana wa Yese, mwana wa Obede, mwana wa Bowazi, mwana wa Salimoni, mwana wa Nasoni, 33mwana wa Aminadabu, mwana wa Admini, mwana wa Arini, mwana wa Hezironi, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda, 34#Gen. 11.24, 26mwana wa Yakobo, mwana wa Isaki, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nahori, 35mwana wa Serugi, mwana wa Reu, mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi, mwana wa Sela, 36mwana wa Kainani, mwana wa Arifaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki, 37mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi, mwana wa Mahalalele, mwana wa Kainani, 38#Gen. 5.1-2mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.
Currently Selected:
LUKA 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi