YouVersion Logo
Search Icon

LUKA 2

2
Kubadwa kwa Yesu Khristu
1Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linatuluka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe; 2#Mac. 5.37ndiko kulembera koyamba pokhala Kwirinio kazembe wa Siriya. 3Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu aliyense kumudzi wake. 4#1Sam. 16.1, 4; Mat. 1.16Ndipo Yosefe yemwe anakwera kuchokera ku Galileya, kumudzi wa Nazarete, kunka ku Yudeya, kumudzi wa Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa iye anali wa banja ndi fuko lake la Davide; 5#Mat. 1.18kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Maria, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati. 6Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala anakwanira. 7#Mat. 1.25Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.
Abusa a ku Betelehemu
8Ndipo panali abusa m'dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang'anira zoweta zao usiku. 9Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha akulu. 10#Gen. 12.3; Mat. 28.19Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse; 11#Yes. 9.6; Mat. 1.16, 21pakuti wakubadwirani inu lero, m'mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye. 12Ndipo ichi ndi chizindikiro kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsalu atagona modyera. 13#Gen. 28.12; Mas. 103.20-21; Aheb. 1.14Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena,
14 # Luk. 19.38; Aro. 5.1; Aef. 2.4, 7 Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba,
ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.
15Ndipo panali, pamene angelo anachokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzake, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye anatidziwitsira ife.
16Ndipo iwo anadza ndi changu, napeza Maria, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera. 17Ndipo iwo, m'mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu. 18Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankhula nao. 19#Gen. 17.12Koma Maria anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwake. 20Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.
Kudulidwa ndi kuperekedwa kwa Yesu
21 # Gen. 17.12; Mat. 1.21, 25 Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba.
22 # Lev. 12.2-8 Ndipo pamene anakwanira masiku a kukonza kwao, monga mwa chilamulo cha Mose, iwo anakwera naye kunka ku Yerusalemu, kukamsonyeza Iye kwa Ambuye, 23#Eks. 13.2(monga mwalembedwa m'chilamulo cha Ambuye, kuti mwamuna aliyense wotsegula pa mimba ya amake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye) 24#Lev. 12.2-8ndi kukapereka nsembe monga mwanenedwa m'chilamulo cha Ambuye, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri.
Za Simeoni ndi za Anna
25 # Yes. 40.1 Ndipo onani, m'Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. 26Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Khristu wake wa Ambuye. 27Ndipo iye analowa ku Kachisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amake analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamchitira Iye mwambo wa chilamulo, 28pomwepo iye anamlandira Iye m'manja mwake, nalemekeza Mulungu, nati,
29 # Afi. 1.23 Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja,
lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere;
30 # Yes. 52.10 chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu,
31chimene munakonza pamaso pa anthu onse,
32 # Yes. 60.1-3 kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu,
ndi ulemerero wa anthu anu Israele.
33Ndipo atate ndi amake anali kuzizwa ndi zinthu zolankhulidwa za Iye. 34#Yes. 8.14; Aro. 9.32-33Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho; 35eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe.
36Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake, 37#1Tim. 5.5zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana. 38#Mrk. 15.43; Luk. 2.25Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu. 39Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, kumudzi kwao, ku Nazarete. 40#Luk. 1.80; 2.52Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.
Mnyamata Yesu pakati pa aphunzitsi
41 # Eks. 23.15, 17 Ndipo atate wake ndi amake akamuka chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku Paska. 42Ndipo pamene Iye anakhala ndi zaka zake khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga machitidwe a chikondwerero; 43ndipo pakumaliza masiku ake, pakubwera iwo, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amake sanadziwe; 44koma iwo anayesa kuti Iye ali m'chipiringu cha ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna Iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao; 45ndipo pamene sanampeze, anabwera ku Yerusalemu, namfunafuna Iye. 46Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye m'Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso. 47#Mat. 7.28; Mrk. 1.22; Luk. 4.22Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake. 48Ndipo m'mene anamuona Iye, anadabwa; ndipo amake anati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa. 49#Yoh. 2.16Ndipo Iye anati kwa iwo, Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna Ine? Simunadziwa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m'zake za Atate wanga? 50#Luk. 9.45Ndipo sanadziwitse mau amene Iye analankhula nao. 51#Luk. 2.19Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.
52 # 1Sam. 2.26 Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.

Currently Selected:

LUKA 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in