Ndipo anamtsogolera Iye ku Yerusalemu, namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisiyo, nati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi; pakuti kwalembedwa kuti,
Adzalamula angelo ake za iwe, kuti akutchinjirize.
Ndipo,
Pa manja ao adzakunyamula iwe,
kuti ungagunde konse phazi lako pamwala.
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa,
Usamuyese Ambuye Mulungu wako.