LUKA Mau Oyamba
Mau Oyamba
Buku la Luka likunena za Yesu monga Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Aisraele komanso Mpulumutsi wa anthu onse. Luka akunena kuti Yesu anaitanidwa ndi Mzimu wa Ambuye kuti, “awuze anthu osauka Uthenga Wabwino” (4.18), ndipo uthengawo ukuonetsa kuti Yesu anali wokhudzidwa ndi anthu amene ali ndi zosowa zosiyanasiyana. Nkhani inanso imene ikuonekera kwambiri mu buku la Luka ndiyo ya chimwemwe. Makamaka izi zikupezeka mu mitu yoyambirira ya bukuli pamene akunena za kubwera kwa Yesu, komanso kumapeto pamene Yesu akukwera kunka kumwamba. Luka analembanso mbiri ya chiyambi ndi kukula kwa mpingo wa Chikhristu Yesu atakwera mu buku lija la Machitidwe.
Bukuli lili ndi magawo awiri (mutu 1—2 ndi 9—19) m'mene muli nkhani zimene zikupezeka mu Luka yekha, nkhanizi ndi monga nyimbo ya angelo ndi ulendo wa abusa kukaona Yesu ali kakhanda, mwana Yesu ali m'Kachisi, ndiponso fanizo la Msamariya wachifundo ndi la Mwana wolowerera. Mu buku lonseli, nkhani yaikulu yagona pa pemphero, Mzimu Woyera, udindo wa azimai pa utumiki wa Yesu komanso kuti Mulungu amakhululukira machimo.
Za mkatimu
Mau oyamba 1.1-4
Kubadwa ndi ubwana wa Yohane Mbatizi komanso Yesu 1.5—2.52
Utumiki wa Yohane Mbatizi 3.1-20
Ubatizo ndi kuyesedwa kwa Yesu 3.21—4.13
Utumiki wa Yesu ku Galileya 4.14—9.50
Kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu 9.51—19.27
Sabata yomaliza mu Yerusalemu ndi madera oyandikira 19.28—23.56
Kuukanso, kuonekera ndi kukwera kumwamba kwa Ambuye 24.1-53
Currently Selected:
LUKA Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi