MARKO 12:41-42
MARKO 12:41-42 BLPB2014
Ndipo Iye anakhala pansi pandunji pa mosungiramo ndalama, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo; ndipo eni chuma ambiri anaponyamo zambiri. Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye anaponyamo tindalama tiwiri tating'ono tokwanira kakobiri kamodzi.