YouVersion Logo
Search Icon

MARKO 12

12
Fanizo la osungira munda
(Mat. 21.33-46; Luk. 20.9-18)
1Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wamphesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina. 2Ndipo m'nyengo yake anatuma kapolo kwa olimawo, kuti alandireko kwa olimawo zipatso za m'munda wamphesa. 3Ndipo iwo anamtenga iye, nampanda, namchotsa wopanda kanthu. 4Ndipo anatumanso kapolo wina kwa iwo; ndipo ameneyu anamlasa mutu, namchitira zomchititsa manyazi. 5Ndipo anatuma wina; iyeyu anamupha; ndi ena ambiri; ena anawapanda, ndi ena anawapha. 6Anamtsalira mmodzi, ndiye mwana wake wokondedwa; potsiriza anamtuma iye kwa iwo, nanena, Adzamchitira ulemu mwana wanga. 7Koma olima ajawo, ananena mwa iwo okha, Ameneyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe iye, ndipo mundawu udzakhala wathu. 8Ndipo anamtenga, namupha iye, namtaya kunja kwa munda. 9Pamenepo mwini munda adzachita chiyani? Adzafika, nadzaononga olimawo, nadzapereka mundawo kwa ena. 10#Mas. 118.22-23Kodi simunawerenga ngakhale lembo ili,
Mwala umene anaukana omanga nyumba,
womwewu unayesedwa mutu wa pangodya:
11Ichi chinachokera kwa Ambuye,
ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?
12Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nachoka.
Za kupereka msonkho
(Mat. 22.15-22; Luk. 20.20-26)
13Ndipo anatuma kwa Iye ena a Afarisi ndi a Aherode, kuti akamkole Iye m'kulankhula kwake. 14Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang'ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai? 15Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa chinyengo chao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga. 16Ndipo ananena nao, Chithunzithunzi ichi, ndi chilembo chake zili za yani? Ndipo anati kwa Iye, Za Kaisara, 17#Aro. 13.7Ndipo Yesu anati kwa iwo, Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo anazizwa naye kwambiri.
Asaduki afunsa za kuuka kwa akufa
(Mat. 22.23-33; Luk. 20.27-40)
18 # Mac. 23.8 Ndipo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye, nanena, 19#Deut. 25.5Mphunzitsi, Mose anatilembera, kuti, Akafa mbale wake wa munthu, nasiya mkazi, wosasiya mwana, mbale wake atenge mkazi wake, namuukitsire mbale wakeyo mbeu. 20Analipo abale asanu ndi awiri; woyamba anakwatira mkazi, nafa, wosasiya mbeu; 21ndipo wachiwiri anamkwatira, nafa, wosasiya mbeu; ndipo wachitatunso anatero momwemo; 22ndipo asanu ndi awiriwo analibe kusiya mbeu. Potsiriza pake pa onse mkazinso anafa. 23Pakuuka adzakhala mkazi wa yani wa iwowa? Pakuti asanu ndi awiriwo adamuyesa mkazi wao. 24Yesu ananena nao, Simusochera nanga mwa ichi, popeza mulibe kudziwa malembo, kapena mphamvu yake ya Mulungu? 25#1Ako. 15.42, 49, 52Pakuti pamene adzauka kwa akufa, sakwatira, kapena sakwatiwa; koma akhala ngati angelo a Kumwamba. Koma za akufa, kuti akaukitsidwa; 26#Eks. 3.6simunawerenga m'buku la Mose kodi, za chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo? 27Sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: musochera inu ndithu.
Lamulo loposa onse
(Mat. 22.34-40)
28Ndipo anadza mmodzi wa alembi, namva iwo alikufunsana pamodzi, ndipo pakudziwa kuti anawayankha bwino, anamfunsa Iye, Lamulo la m'tsogolo la onse ndi liti? 29#Deut. 6.4; Luk. 10.27Yesu anayankha, kuti, La m'tsogolo ndili, Mvera, Israele; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi; 30ndipo uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse. 31#Lev. 19.8; Mat. 22.39; Aro. 13.9; Agal. 5.14Lachiwiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa. 32#Deut. 4.39Ndipo mlembiyo anati kwa Iye, Chabwino, Mphunzitsi, mwanena zoona kuti ndiye mmodzi; ndipo palibe wina, koma Iye: 33#1Sam. 15.22; Hos. 6.6ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzake monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa. 34#Mat. 22.46Ndipo pakuona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kumfunsa Iye kanthu.
Khristu mwana wa Davide
(Mat. 22.41-46; Luk. 20.41-44)
35Ndipo Yesu pamene anaphunzitsa m'Kachisi, anayankha, nanena, Bwanji alembi anena kuti Khristu ndiye mwana wa Davide? 36#Mas. 110.1Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako. 37Davide mwini yekha amtchula Iye Ambuye; ndipo ali mwana wake bwanji? Ndipo anthu a makamuwo anakondwa kumva Iye.
Yesu awachenjeza za Alembi
(Mat. 23.1-12; Luk. 20.45-47)
38 # Luk. 11.43; 20.46 Ndipo m'chiphunzitso chake ananena, Yang'anirani mupewe alembi, akufuna kuyendayenda ovala miinjiro, ndi kulonjeredwa pamisika, 39ndi kukhala nayo mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando: 40amenewo alusira nyumba za akazi amasiye, napemphera monyenga mau ambiri; amenewa adzalandira kulanga koposa.
Mphatso ya mkazi wamasiye
(Luk. 21.1-4)
41 # 2Maf. 12.9 Ndipo Iye anakhala pansi pandunji pa mosungiramo ndalama, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo; ndipo eni chuma ambiri anaponyamo zambiri. 42Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye anaponyamo tindalama tiwiri tating'ono tokwanira kakobiri kamodzi. 43#2Ako. 8.12Ndipo anaitana ophunzira ake, nati kwa iwo, Ndithu ndinena ndi inu, Mkazi wamasiye amene waumphawi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo: 44pakuti anaponyamo onse mwa zochuluka zao; koma iye anaponya mwa kusowa kwake zonse anali nazo, inde moyo wake wonse.

Currently Selected:

MARKO 12: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in