MARKO 13
13
Yesu aneneratu za masautso alinkudza
(Mat. 24.1-14; Luk. 21.5-19)
1Ndipo pamene analikutuluka Iye m'Kachisi, mmodzi wa ophunzira ake ananena kwa Iye, Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere. 2#Luk. 19.44Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikulu? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzake, umene sudzagwetsedwa.
3Ndipo pamene anakhala Iye pa phiri la Azitona, popenyana ndi Kachisi, anamfunsa Iye m'tseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Andrea, kuti, 4#Luk. 21.7Tiuzeni, zinthu izi zidzachitika liti? Ndi chotani chizindikiro chake chakuti zili pafupi pa kumalizidwa zinthu izi zonse? 5#Yer. 29.8; Aef. 5.6Ndipo Yesu anayamba kunena nao, Yang'anirani kuti munthu asakusocheretseni. 6Ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasocheretsa ambiri. 7Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenera kuchitika izi; koma sichinafike chimaliziro. 8Pakuti mtundu wa anthu udzayambana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu unzake: padzakhala zivomezi m'malo m'malo; padzakhala njala; izi ndi zoyambira za zowawa.
9 #
Mat. 10.17-19; Luk. 21.14-16 Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo. 10Ndipo Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. 11#Mat. 10.17-19; Luk. 21.14-16; Mac. 4.8, 31Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musade nkhawa usanayambe mlandu ndi chimene mudzalankhula; koma chimene chidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, muchilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera. 12#Mik. 7.6; Mat. 10.21Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuti amuphe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzayambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa. 13#Luk. 21.17Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa: koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa.
Yesu aneneratu za chisautso chachikulu
(Mat. 24.15-28; Luk. 21.20-24)
14Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a m'Yudeya athawire kumapiri: 15ndi iye amene ali pamwamba pa chindwi asatsike, kapena asalowe kukatulutsa kanthu m'nyumba mwake; 16ndi iye amene ali kumunda asabwere kudzatenga malaya ake. 17#Luk. 21.23; 23.29Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana masiku awo! 18Ndipo pempherani kuti kusakhale m'nyengo yachisanu. 19Pakuti masiku aja padzakhala chisautso, chonga sichinakhala chinzake kuyambira chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu anachilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sichidzakhalanso, nthawi zonse. 20Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma chifukwa cha osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo. 21#Luk. 17.23; 21.8Ndipo pamenepo wina akati kwa inu, Onani Khristu ali pano; kapena, Onani, uko; musavomereze; 22pakuti adzauka Akhristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe. 23#2Pet. 3.17Koma yang'anirani; onani ndakuuziranitu zinthu zonse, zisanafike.
Yesu aneneratu kuti adzabwera
(Mat. 24.29-36; Luk. 21.25-33)
24 #
Zef. 1.15
Koma m'masikuwo, chitatha chisautso chimenecho, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwake, 25ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera m'mwamba ndi mphamvu zili m'mwamba zidzagwedezeka. 26#Dan. 7.13-14; Mat. 16.27; Mrk. 14.62; Mac. 1.11; 1Ate. 4.16; Chiv. 1.7Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa Munthu alinkudza m'mitambo ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemerero. 27Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake ochokera kumphepo zinai, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.
28 #
Luk. 21.29-30
Ndipo phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene pafika kuti nthambi yake ikhala yanthete, ndipo anaphuka masamba ake, muzindikira kuti layandikira dzinja; 29chomwecho inunso, pamene muona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti ali pafupi pakhomo. 30Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu izi zonse zitachitika. 31#Yes. 40.8Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita. 32Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yake sadziwa munthu, angakhale angelo m'Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye.
Za kulindirira
(Mat. 24.36-44; Luk. 21.34-36)
33 #
Mat. 25.13; Luk. 12.40 Yang'anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yake. 34#Mat. 25.14Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamula wapakhomo adikire. 35Chifukwa chake dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yake yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa; 36kuti angabwere balamanthu nakakupezani muli m'tulo. 37Ndipo chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.
Currently Selected:
MARKO 13: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi