Chifukwa chake dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yake yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa; kuti angabwere balamanthu nakakupezani muli m'tulo. Ndipo chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.