MARKO 11
11
Yesu alowa m'Yerusalemu alikukhala pa bulu
(Mat. 21.1-11; Luk. 19.29-44; Yoh. 12.12-19)
1Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri la Azitona, anatuma awiri a ophunzira ake, 2nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye. 3Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno. 4Ndipo anachoka, napeza mwana wa bulu womangidwa pakhomo, pabwalo m'khwalala, nammasula iye. 5Ndipo ena akuima kumeneko ananena nao, Muchita chiyani ndi kumasula mwana wa bulu? 6Ndipo anati kwa iwo monga momwe ananena Yesu: ndipo anawalola iwo apite naye. 7Ndipo anabwera naye mwana wa bulu kwa Yesu, naika zovala zao pa iye, ndipo Iye anakhala pamenepo. 8Ndimo ambiri anayala zovala zao panjira; ndi ena zitsamba, anazidula m'minda. 9#Mas. 118.26Ndipo akutsogolera, ndi iwo akutsata, anafuula, Hosana; Wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye: 10#Mas. 148.1Wolemekezeka Ufumu ulinkudza, wa atate wathu Davide; Hosana m'Kumwambamwamba.
11 #
Mat. 21.12
Ndipo Iye analowa m'Yerusalemu, m'Kachisi; ndipo m'mene anaunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.
Yesu atemberera mkuyu
(Mat. 21.18-22)
12Ndipo m'mawa mwake, atatuluka ku Betaniya, Iye anamva njala. 13Ndipo anaona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m'mene anafikako anapeza palibe kanthu koma masamba okha; pakuti siinali nyengo yake ya nkhuyu. 14Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ake anamva.
Yesu atulutsa amalonda m'Kachisi
(Mat. 21.12-17; Luk. 19.45-48)
15 #
Yoh. 2.14
Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kachisi, nayamba kutulutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kachisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda; 16ndipo sanalole munthu aliyense kunyamula chotengera kupyola pakati pa Kachisi. 17#Yes. 56.7; Yer. 7.11Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sichilembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? Koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba. 18#Luk. 19.47; Mat. 7.28Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, chifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.
19Ndipo masiku onse madzulo anatuluka Iye m'mudzi.
Mkuyu wouma
(Mat. 21.18-22)
20Ndipo m'mene anapitapo m'mawa mwake, anaona kuti mkuyu uja unafota, kuyambira kumizu. 21Ndipo Petro anakumbukira, nanena naye, Rabi, onani, wafota mkuyuwo munautemberera. 22Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu. 23#Mat. 17.20; 21.21; Luk. 17.6Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu aliyense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwake, koma adzakhulupirira kuti chimene achinena chichitidwa, adzakhala nacho. 24#Mat. 7.7; Yoh. 14.13; 15.7; Yak. 1.5-6Chifukwa chake ndinena ndi inu, Zinthu zilizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo. 25#Mat. 6.14; Akol. 3.13Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu.#11.25 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 26 Mukapanda inu kukhululukira anzanu, Atate anunso wa Kumwamba sadzakhululukira inu machimo anu.
Ubatizo wa Yohane
(Mat. 21.23-27; Luk. 20.1-8)
27Ndipo iwo anadzanso ku Yerusalemu; ndipo m'mene Iye anali kuyenda m'Kachisi, anafika kwa Iye ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu; 28nanena naye, Izi muzichita ndi ulamuliro wotani? Kapena anakupatsani ndani ulamuliro uwu wakuchita izi? 29Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani mau amodzi, mundiyankhe Ine, ndipo ndidzakuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu zimenezi. 30Ubatizo wa Yohane uchokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu? Mundiyankhe. 31Ndipo anatsutsana mwa iwo okha, nanena, Tikati, Kumwamba; adzanena Iye, Ndipo simunakhulupirira iye bwanji? 32#Mat. 14.5Koma tikati, Kwa anthu, anaopa anthuwo; pakuti onse anamuyesa Yohane mneneri ndithu. 33Ndipo iwo anamyankha Yesu, ananena nao, Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu zimenezi.
Currently Selected:
MARKO 11: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi