MARKO 10
10
Asasiyane mwamuna ndi mkazi wake
(Mat. 19.1-12)
1 #
Yoh. 10.40
Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordani; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso. 2#Mat. 19.3Ndipo anadza kwa Iye Afarisi, namfunsa Iye ngati kuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake, namuyesa Iye. 3Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi Mose anakulamulani chiyani? 4#Deut. 24.1; Mat. 5.31; 19.7Ndipo anati, Mose analola kulembera kalata wakulekanira, ndi kumchotsa. 5Koma Yesu anati kwa iwo, Chifukwa cha kuuma kwa mitima yanu anakulemberani lamulo ili. 6#Gen. 1.27Koma kuyambira pa chiyambi cha malengedwe anawapanga mwamuna ndi mkazi. 7#Gen. 2.24; 1Ako. 6.16; Aef. 5.31Chifukwa chake mwamuna adzasiya atate wake ndi amai wake, ndipo adzaphatikizana ndi mkazi wake; 8#Gen. 2.24; 1Ako. 6.16; Aef. 5.31ndipo awiriwa adzakhala thupi limodzi: kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. 9Chifukwa chake chimene Mulungu anachimanga pamodzi, asachilekanitse munthu. 10Ndipo m'nyumba ophunzira anamfunsanso za chinthu ichi. 11#Mat. 5.32; 19.9; Luk. 16.18; Aro. 7.3; 1Ako. 7.10-11Ndipo Iye ananena nao, Munthu aliyense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo; 12ndipo ngati mkazi akachotsa mwamuna wake, nakwatiwa ndi wina, achita chigololo iyeyu.
Yesu adalitsa tiana
(Mat. 19.13-15; Luk. 18.15-17)
13Ndipo analinkudza nato kwa Iye tiana, kuti akatikhudze; ndipo ophunzirawo anawadzudzula. 14#1Ako. 14.20; 1Pet. 2.2Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere. 15Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse. 16Ndipo Iye anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ake pa ito.
Mnyamata mwini chuma chambiri
(Mat. 19.16-30; Luk. 18.18-30)
17Ndipo pamene Iye anatuluka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha? 18Ndipo Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu. 19#Eks. 20.14; Aro. 13.9Udziwa malamulo: Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amai ako. 20Ndipo iye anati kwa Iye, Mphunzitsi, zonsezi ndinazisunga kuyambira ndili mwana. 21#Mat. 6.19-20; Luk. 12.33Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Chinthu chimodzi chikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo chuma udzakhala nacho m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine. 22Koma nkhope yake inagwa pa mau awa, ndipo anachoka iye wachisoni; pakuti anali mwini chuma chambiri. 23#Luk. 18.24Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ake, Okhala nacho chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga! 24#Mas. 52.7; 1Tim. 6.17Ndipo ophunzirawo anazizwa ndithu ndi mau ake. Koma Yesu anayankhanso nanena nao, Ananu, nkovuta ndithu kwa iwo akutama chuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu! 25Nkwa pafupi kuti ngamira ipyole diso la singano kuposa kuti mwini chuma alowe mu Ufumu wa Mulungu. 26Ndipo anadabwa, nanena kwa Iye, Ndipo angathe kupulumuka ndani? 27#Yer. 32.17Yesu anawayang'ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu. 28#Luk. 18.28Petro anayamba kunena naye, Onani, ife tinasiya zonse, ndipo tinakutsatani Inu. 29Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwinowo, 30#2Mbi. 25.9; Luk. 18.30amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthawi yino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amai, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthawi ilinkudza, moyo wosatha. 31#Luk. 13.30Koma ambiri akuyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.
Ali panjira kukwera ku Yerusalemu
(Mat. 20.17-19; Luk. 18.31-34)
32 #
Mrk. 8.31; 9.31; Luk. 9.22; 18.31 Ndipo iwo anali m'njira alinkukwera kunka ku Yerusalemu; ndipo Yesu analikuwatsogolera; ndipo iwo anazizwa; ndipo akumtsatawo anachita mantha. Ndipo Iye anatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwauza zinthu zimene zidzamfikira Iye, 33nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu; 34ndipo adzamnyoza Iye, nadzamthira malovu, nadzamkwapula Iye, nadzamupha; ndipo pofika masiku atatu adzauka.
Ana a Zebedeo apempha ulemu
(Mat. 20.20-28)
35Ndipo anadza kwa Iye Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, nanena naye, Mphunzitsi, tifuna kuti mudzatichitire chimene chilichonse tidzapempha kwa Inu. 36Ndipo Iye anati kwa iwo, Mufuna kuti ndidzakuchitireni inu chiyani? 37Ndipo iwo anati kwa Iye, Mutipatse ife kuti tikhale mmodzi kudzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, m'ulemerero wanu. 38Koma Yesu anati kwa iwo, Simudziwa chimene muchipempha. Mukhoza kodi kumwera chikho chimene ndimwera Ine? Kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine? 39Ndipo anati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Chikho chimene ndimwera Ine mudzamwera; ndipo ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine, mudzabatizidwa nao; 40koma kukhala kudzanja langa lamanja, kapena lamanzere sikuli kwanga kupatsa; koma kuli kwa iwo amene adawakonzeratu. 41Ndipo pamene khumiwo anamva, anayamba kupsa mtima chifukwa cha Yakobo ndi Yohane. 42#Luk. 22.25Ndipo Yesu anawaitana, nanena nao, Mudziwa kuti iwo amene ayesedwa ambuye a mitundu ya anthu amachita ufumu pa iwo; ndipo akulu ao amachita ulamuliro pa iwo. 43#Luk. 9.48Koma mwa inu sikutero ai; koma amene aliyense afuna kukhala wamkulu mwa inu adzakhala mtumiki wanu; 44ndipo amene aliyense afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala kapolo wa onse. 45#Yoh. 13.14; Afi. 2.7; 1Tim. 2.6Pakuti ndithu, Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.
Baratimeo wakhungu wa ku Yeriko
(Mat. 20.29-34; Luk. 18.35-43)
46Ndipo iwo anafika ku Yeriko; ndipo m'mene Iye analikutuluka m'Yeriko, ndi ophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu, mwana wa Timeo, Baratimeo, wopempha wakhungu, analikukhala pansi m'mbali mwa njira. 47Ndipo pamene anamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, anayamba kufuula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundichitire ine chifundo. 48Ndipo ambiri anamulamula kuti atonthole: koma makamaka anafuulitsa kuti, Inu mwana wa Davide, mundichitire chifundo. 49Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana. 50Ndipo iye anataya chofunda chake, nazunzuka, nadza kwa Yesu. 51Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikuchitire chiyani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga. 52#Mat. 9.22; Mrk. 5.34Ndipo Yesu anati kwa iye, Muka; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso; namtsata Iye panjira.
Currently Selected:
MARKO 10: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi