YouVersion Logo
Search Icon

MARKO 9

9
Mawalitsidwe a Yesu paphiri
(Mat. 17.1-13; Luk. 9.28-36)
1 # Mat. 16.28; Luk. 9.27 Ndipo ananena nao, Ndithu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira akaona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.
2Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao pa phiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao: 3ndipo zovala zake zinakhala zonyezimira, zoyera mbu; monga ngati muomba wotsuka nsalu pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsai. 4Ndipo anaonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikulankhulana ndi Yesu. 5Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya. 6Pakuti sanadziwe chimene adzayankha; chifukwa anachita mantha ndithu. 7Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munatuluka m'mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye. 8Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenye munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.
9Ndipo pakutsika iwo paphiri, Iye anawalamula kuti asauze munthu zinthu zimene adaziona, koma pamene Mwana wa Munthu akadzauka kwa akufa. 10Ndipo anasunga mauwo, nafunsana mwa iwo okha, kuti, Kuuka kwa akufa nchiyani? 11#Mala. 4.5Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Nanga alembi anena kuti adzayamba kufika Eliya? 12#Mas. 22.6; Yes. 53Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa Munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa chabe? 13#Mat. 11.14Koma ndinena ndi inu kuti anafikadi Eliya, ndipo anamchitiranso zilizonse iwo anazifuna, monga kwalembedwa za iye.
Achiritsidwa mwana wogwidwa ndi mzimu wosalankhula
(Mat. 17.14-20; Luk. 9.37-43)
14Ndipo pamene anadza kwa ophunzira, anaona khamu lalikulu la anthu ozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nao. 15Ndipo pomwepo anthu onse a khamulo, pakumuona Iye, anazizwa kwambiri, namthamangira Iye, namlonjera. 16Ndipo anawafunsa iwo, Mufunsana nao chiyani? 17#Luk. 9.38Ndipo wina wa m'khamulo anamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nao mzimu wosalankhula; 18ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti autulutse; koma sanakhoze. 19Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine. 20#Mrk. 1.26; Luk. 9.42Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng'amba koopsa; ndipo anagwa pansi navimvinika ndi kuchita thovu. 21Ndipo Iye anafunsa atate wake, kuti, Chimenechi chinayamba kumgwira liti? Ndipo anati, Chidamyamba akali mwana. 22Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo. 23#Mrk. 11.23; Luk. 17.6; Yoh. 11.40Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira. 24Pomwepo atate wa mwana anafuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga. 25Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye. 26Ndipo pamene unafuula, numng'ambitsa, unatuluka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira. 27Koma Yesu anamgwira dzanja lake, namnyamutsa; ndipo anaimirira. 28Ndipo pamene Iye adalowa m'nyumba, ophunzira ake anamfunsa m'tseri, kuti, Nanga bwanji sitinakhoza ife kuutulutsa? 29Ndipo Iye anati kwa iwo, Mtundu uwu sukhoza kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.
Wamkulu ndani m'Ufumu wa Mulungu?
(Mat. 18.1-14; Luk. 9.43-48)
30Ndipo anachoka iwo kumeneko, napyola pakati pa Galileya; ndipo Iye sanafune kuti munthu adziwe. 31#Mat. 17.22; Luk. 9.44Pakuti anaphunzitsa ophunzira ake, nanena nao, kuti, Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu. 32Koma iwo sanazindikire mauwo, naopa kumfunsa.
33 # Luk. 22.24 Ndipo iwo anadza ku Kapernao; ndipo pamene anakhala m'nyumba, Iye anawafunsa, Munalikutsutsana ninji panjira? 34Koma iwo anakhala chete; pakuti anatsutsana wina ndi mnzake panjira, kuti, wamkulu ndani? 35#Mat. 20.26-27; Mrk. 10.43-44Ndipo m'mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse. 36#Mrk. 10.16Ndipo anatenga kamwana, nakaika pakati pao, nakayangata, nanena nao, 37#Mat. 10.40; Luk. 9.48Munthu aliyense adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.
Osatsutsana nafe athandizana nafe
(Luk. 9.49-50)
38Yohane anati kwa Iye, Mphunzitsi, tinaona munthu alikutulutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa sanalikutsata ife. 39#1Ako. 12.3Koma Yesu anati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzachita champhamvu m'dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoipa. 40Pakuti iye wosatsutsana ndi ife athandizana nafe. 41#Mat. 10.42Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m'dzina langa chifukwa muli ake a Khristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake.
Malakwitso
(Mat. 18.6-10; Luk. 17.1-4)
42Ndipo yense amene adzalakwitsa kamodzi ka tiana timeneto takukhulupirira Ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wamphero ukolowekedwe m'khosi mwake, naponyedwe iye m'nyanja. 43#Mat. 5.29; 18.8-9Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: nkwabwino kwa iwe kulowa m'moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa m'Gehena, m'moto wosazima.#9.43 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 44 Kumeneko mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima. 45Ndipo ngati phazi lako likulakwitsa, ulidule; kulowa iwe m'moyo wopunduka mwendo, kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi mapazi ako awiri ndi kuponyedwa m'Gehena.#9.45 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 46 Kumeneko mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima. 47#Mat. 5.29; 18.8-9Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe m'Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa m'Gehena; 48kumeneko mphutsi yao siikufa, ndi moto suzimidwa. 49Pakuti onse adzathiridwa mchere wamoto. 50#Mat. 5.13; Luk. 14.34; Aro. 12.18; 2Ako. 13.11; Akol. 4.6; Aheb. 12.14Mchere uli wabwino; koma ngati mchere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi chiyani? Khalani nao mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake.

Currently Selected:

MARKO 9: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in