YouVersion Logo
Search Icon

MARKO 8

8
Yesu achulukitsa mikate kachiwiri
(Mat. 15.32-39; Mrk. 6.32-44)
1Masiku ajawo pakukhalanso khamu lalikulu la anthu, ndipo analibe kanthu kakudya, Iye anadziitanira ophunzira ake, nanena nao, 2Ndimva nalo chifundo khamulo, chifukwa ali ndi Ine chikhalire masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya: 3ndipo ngati ndiwauza iwo amuke kwao osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena a iwo achokera kutali. 4Ndipo ophunzira ake anamyankha Iye, kuti, Munthu adzatha kutenga kuti mikate yakukhutitsa anthu awa m'chipululu muno? 5#Mat. 15.34Ndipo anawafunsa, Muli nayo mikate ingati? Ndipo anati, Isanu ndi iwiri. 6Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ake, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo. 7#Mat. 14.19; Mrk. 6.41Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso. 8Ndipo anadya nakhuta; ndipo anatola makombo madengu asanu ndi awiri. 9Ndipo iwo anali ngati zikwi zinai; ndipo Iye analawirana nao. 10#Mat. 15.39Ndipo pomwepo analowa m'ngalawa ndi ophunzira ake, nafika ku mbali ya ku Dalamanuta.
Afarisi afuna chizindikiro
(Mat. 16.1-4)
11 # Yoh. 6.30 Ndipo Afarisi anatuluka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba, namuyesa Iye. 12Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno! 13Ndipo anawasiya iwo, nalowanso m'ngalawa, nachoka kunka ku tsidya lija.
Chotupitsa mkate cha Afarisi
(Mat. 16.5-12; Luk. 12.1)
14Ndipo ophunzira adaiwala kutenga mikate, ndipo analibe mkate m'ngalawa koma umodzi wokha. 15#Mat. 16.6Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode. 16#Mat. 16.7Ndipo anatsutsana wina ndi mnzake, nanena kuti, Tilibe mikate. 17#Mrk. 6.52Ndipo Yesu pamene anazindikira, ananena nao, Bwanji mutsutsana chifukwa mulibe mkate? Kodi kufikira tsopano simuzindikira, nisimudziwitsa? Kodi muli nayo mitima yanu youma? 18Pokhala nao maso simupenya kodi? Ndi pokhala nao makutu simukumva kodi? Ndipo simukumbukira kodi? 19#Mat. 14.20Pamene ndinawagawira anthu zikwi zisanu mikate isanu ija, munatola madengu angati odzala ndi makombo? Ananena naye, Khumi ndi iwiri. 20#Mat. 15.37Ndipo mikate isanu ndi iwiri kwa anthu zikwi zinai, munatola madengu angati odzala ndi makombo? Ndipo ananena naye, Asanu ndi awiri. 21#Mrk. 8.17Ndipo Iye ananena nao, Simudziwitsa ngakhale tsopano kodi?
Yesu achiritsa munthu wakhungu ku Betsaida
22Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze. 23#Mrk. 7.33Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malovu m'maso mwake, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi? 24Ndipo anakweza maso, nanena, Ndiona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo. 25Pamenepo anaikanso manja m'maso mwake; ndipo anapenyetsa, nachiritsidwa, naona zonse mbee. 26Ndipo anamtumiza amuke kwao, nanena, Usalowe konse m'mudzi.
Petro avomereza Khristu
(Mat. 16.13-23; Luk. 9.18-22; Yoh. 6.66-69)
27Ndipo anatuluka Yesu, ndi ophunzira ake, nalowa kumidzi ya ku Kesareya-Filipi; ndipo panjira anafunsa ophunzira ake, nanena nao, Kodi anthu ananena kuti Ine ndine yani? 28#Mat. 14.2Ndipo ananena, nati, Yohane Mbatizi; ndi ena, Eliya; koma ena, Mmodzi wa aneneri. 29#Yoh. 11.27Ndipo Iye anawafunsa, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro anayankha nanena naye, Ndinu Khristu. 30Ndipo anawauzitsa iwo kuti asanene kwa munthu mmodzi za Iye. 31#Mat. 17.22-23; Luk. 9.22Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa Munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke. 32Ndipo mauwo ananena poyera. Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula. 33Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ake, namdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.
Kunyamula mtanda
(Mat. 16.24-28; Luk. 9.23-27)
34 # Mat. 10.38; Luk. 14.27 Ndipo anadziitanira khamulo la anthu pamodzi ndi ophunzira ake, nati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake, nanditsate Ine. 35#Yoh. 12.25Pakuti yense wakufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya; ndipo yense wakutaya moyo wake chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa. 36Pakuti munthu apindulanji akadzilemezera dziko lonse, natayapo moyo wake? 37Pakuti munthu akapereka chiyani chosintha nacho moyo wake? 38#Mat. 10.33; Luk. 9.26; 12.9; Aro. 1.16; 2Tim. 1.8Pakuti yense wakuchita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mau anga mu mbadwo uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika nao angelo ake oyera, mu ulemerero wa Atate wake.

Currently Selected:

MARKO 8: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in