YouVersion Logo
Search Icon

MARKO 15

15
Yesu aweruzidwa ndi Pilato
(Mat. 27.1-2, 11-31; Luk. 23.1-25; Yoh. 18.28—19.16)
1 # Mas. 2.2; Mac. 3.13 Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato. 2Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero. 3Ndipo ansembe aakulu anamnenera Iye zinthu zambiri. 4Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere. 5#Yes. 53.7Koma Yesu sanayankhenso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa.
6Ndipo ankawamasulira pachikondwerero wandende mmodzi, amene iwo anampempha. 7Ndipo analipo wina dzina lake Barabasi, wamangidwa pamodzi ndi opanduka, amene anapha munthu mumphandumo. 8Ndipo khamu la anthu anabwera nayamba kupempha kuti achite monga anali kuwachitira nthawi zonse. 9Ndipo Pilato anawayankha, nanena nao, Kodi mufuna kuti ndikumasulireni mfumu ya Ayuda? 10Pakuti anazindikira kuti ansembe aakulu anampereka Iye mwanjiru. 11#Mac. 3.14Koma ansembe aakulu anasonkhezera khamulo, kuti makamaka awamasulire Barabasi. 12Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzachita chiyani ndi Iye amene mumtchula mfumu ya Ayuda? 13Ndipo anafuulanso, Mpachikeni pamtanda. 14Ndipo Pilato ananena nao, Pakuti Iye anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsatu, Mpachikeni Iye. 15Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Barabasi, napereka Yesu, atamkwapula, akampachike pamtanda.
16Ndipo asilikali anachoka naye nalowa m'bwalo, ndilo Pretorio; nasonkhanitsa gulu lao lonse. 17Ndipo anamveka Iye chibakuwa, naluka korona waminga, namveka pa Iye; 18Ndipo anayamba kumlankhula Iye, kuti, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda! 19Ndipo anampanda Iye pamutu pake ndi bango, namthira malovu, nampindira maondo, namlambira. 20Ndipo atatha kumnyoza anamvula chibakuwacho namveka Iye zovala zake. Ndipo anatuluka naye kuti akampachike Iye pamtanda.
Ampachika Yesu pamtanda
(Mat. 27.32-56; Luk. 23.26-49; Yoh. 19.17-37)
21Ndipo anakakamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, atate wao wa Aleksandro ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wake. 22#Luk. 23.33Ndipo anamtenga kunka naye kumalo Gologota, ndiwo, osandulika, Malo a Bade. 23Ndipo anampatsa vinyo wosanganiza ndi mure; koma Iye sanamlandire. 24#Mas. 22.18; Luk. 23.34Ndipo anampachika Iye, nagawana zovala zake mwa iwo okha, ndi kuchita maere pa izo, kuti adziwe yense adzatenga chiyani. 25Ndipo panali ora lachitatu, ndipo anampachika Iye. 26Ndipo lembo la mlandu wake linalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA. 27Ndipo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri; mmodzi kudzanja lake lamanja ndi wina kulamanzere.#15.27 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 28 Motero linakwaniritsidwa lemba lakuti, “Ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa.” 29#Mas. 22.7; Mrk. 14.58; Yoh. 2.19Ndipo iwo akupitirirapo anamchitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! Iwe wakupasula Kachisi, ndi kummanga masiku atatu, 30udzipulumutse mwini, nutsike pamtanda. 31Moteronso ansembe aakulu anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sakhoza kudzipulumutsa yekha. 32Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.
33 # Luk. 23.44-49 Ndipo pofika ora lachisanu ndi chimodzi, panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai. 34#Mas. 22.1Ndipo pa ora lachisanu ndi chinai Yesu anafuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika,
Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?
35Ndipo ena akuimirirapo, pakumva, ananena, Taonani, aitana Eliya. 36#Mas. 69.21Ndipo anathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye, nanena, Lekani; tione ngati Eliya adza kudzamtsitsa. 37Ndipo Yesu anatulutsa mau okweza, napereka mzimu wake. 38#Luk. 23.44-49Ndipo chinsalu chotchinga cha m'Kachisi chinang'ambika pakati, kuyambira kumwamba kufikira pansi. 39#Luk. 23.44-49Ndipo pamene kenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu. 40#Mas. 38.11; Mrk. 16.1; Luk. 23.44-49Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yosefe, ndi Salome; 41#Luk. 8.2-3amene anamtsata Iye, pamene anali m'Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu.
Yesu aikidwa m'manda
(Mat. 27.57-66; Luk. 23.50-56; Yoh. 19.38-42)
42Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzekera, ndilo la pambuyo pa Sabata, 43#Luk. 2.25, 38anadzapo Yosefe wa ku Arimatea, mkulu wa milandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wake wa Yesu. 44Ndipo Pilato anazizwa ngati adamwaliradi; naitana kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale. 45Ndipo pamene anachidziwa ndi kenturiyo, anamninkha Yosefe mtembowo. 46#Luk. 23.53Ndipo anagula bafuta, namtsitsa Iye, namkulunga m'bafutamo, namuika m'manda osemedwa m'thanthwe; nakunkhunizira mwala pakhomo la manda. 47Ndipo Maria wa Magadala ndi Maria amake wa Yosefe anapenya pomwe anaikidwapo.

Currently Selected:

MARKO 15: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in