YouVersion Logo
Search Icon

AROMA 2

2
Kusamvera kwa Ayuda
1 # 2Sam. 12.5-7; Mat. 7.1-2; Yoh. 8.9 Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo. 2Ndipo tidziwa kuti kuweruza kwa Mulungu kuli koona pa iwo akuchita zotere.
3Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zotere, ndipo uzichitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa mlandu wa Mulungu? 4#Yes. 30.18; Aro. 3.25Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape? 5#Yak. 5.3Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu; 6#Mas. 62.12; Mat. 16.27amene adzabwezera munthu aliyense kolingana ndi ntchito zake; 7kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha; 8#2Ate. 1.8koma kwa iwo andeu, ndi osamvera choonadi, koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza, 9#Amo. 3.2; Luk. 12.47-48nsautso ndi kuwawa mtima, kwa moyo wa munthu aliyense wakuchita zoipa, kuyambira Myuda, komanso Mgriki; 10koma ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino, kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki; 11#Deut. 10.17; Mac. 10.34pakuti Mulungu alibe tsankho. 12Pakuti onse amene anachimwa opanda lamulo adzaonongeka opanda lamulo; ndi onse amene anachimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo; 13#Mat. 7.21; Yak. 1.22-25pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama. 14Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; 15popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo chikumbu mtima chao chichitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana; 16#Mat. 25.31-32tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.
Ayuda atsutsidwa
17Koma ngati iwe unenedwa Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu, 18nudziwa chifuniro chake, nuvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m'chilamulo, 19#Mat. 23.16-17, 19, 24nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima, 20wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m'chilamulo ndi chionekedwe cha nzeru ndi cha choonadi; 21#Mas. 50.16; Mat. 23.3ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? 22Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za m'Kachisi kodi? 23Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'chilamulo? 24#Ezk. 36.20, 23Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.
Mdulidwe woona
25 # Agal. 5.3 Pakuti inde mdulidwe uli wabwino, ngati iwe umachita lamulo; koma ngati uli wolakwira lamulo, mdulidwe wako wasanduka kusadulidwa. 26#Mac. 10.34-35Chifukwa chake ngati wosadulidwa asunga zoikika za chilamulo, kodi kusadulidwa kwake sikudzayesedwa ngati mdulidwe? 27#Mat. 12.41-42Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa chibadwidwe, ngati kukwanira chilamulo, kodi sikudzatsutsa iwe, amene uli nao malembo ndi mdulidwe womwe, ndiwe wolakwira lamulo? 28#Yoh. 8.39Pakuti siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m'thupimo; 29#1Pet. 3.4; Akol. 2.11koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.

Currently Selected:

AROMA 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in