AROMA 4
4
Abrahamu anayesedwa wolungama ndi chikhulupiriro
1Ndipo tsono tidzanena kuti Abrahamu, kholo lathu monga mwa thupi, analandira chiyani? 2Pakuti ngati Abrahamu anayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito, iye akhala nacho chodzitamandira; koma kulinga kwa Mulungu ai. 3#Gen. 15.6; Agal. 3.6Pakuti lembo litani? Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo chinawerengedwa kwa iye chilungamo. 4#Aro. 11.6Ndipo kwa iye amene agwira ntchito, mphotho siiwerengedwa ya chisomo koma ya mangawa. 5Koma kwa iye amene sachita, koma akhulupirira Iye amene ayesa osapembedza ngati olungama, chikhulupiriro chake chiwerengedwa chilungamo. 6Monganso Davide anena za mdalitso wake wa munthu, amene Mulungu amwerengera chilungamo chopanda ntchito, 7#Mas. 32.1-2ndi kuti,
Odala iwo amene akhululukidwa kusaweruzika kwao,
nakwiriridwa machimo ao.
8Wodala munthu amene Mulungu samwerengera uchimo.
9Mdalitso umenewu tsono uli kwa odulidwa kodi, kapena kwa osadulidwa omwe? Pakuti timati, Chikhulupiriro chake chinawerengedwa kwa Abrahamu chilungamo. 10Tsono chinawerengedwa bwanji? M'mene iye anali wodulidwa kapena wosadulidwa? Si wodulidwa ai, koma wosadulidwa; 11#Gen. 17.10-11; Luk. 19.9iye ndipo analandira chizindikiro cha mdulidwe, ndicho chosindikiza chilungamo cha chikhulupiriro, chomwe iye anali nacho asanadulidwe; kuti kotero iye akhale kholo la onse akukhulupirira, angakhale iwo sanadulidwa, kuti chilungamo chiwerengedwe kwa iwonso; 12ndiponso kholo la mdulidwe wa iwo amene siali a mdulidwe okha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe a chikhulupiriro chija cha kholo lathu Abrahamu, chimene iye anali nacho asanadulidwe. 13#Agal. 3.29Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowa nyumba wa dziko lapansi silinapatsidwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake mwa lamulo, koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro. 14#Agal. 3.18Pakuti ngati iwo a lamulo akhala olowa nyumba, pamenepo chikhulupiriro chayesedwa chabe, ndimo lonjezo layesedwa lopanda pake; 15#Agal. 3.10, 19pakuti chilamulo chichitira mkwiyo; koma pamene palibe lamulo, pamenepo palibe kulakwa. 16#Aro. 3.24; Agal. 3.22Chifukwa chake chilungamo chichokera m'chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbeu zonse; si kwa iwo a chilamulo okhaokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye kholo la ife tonse; 17#Gen. 17.5; Aef. 2.1, 5monga kwalembedwa: Ndinakukhazika iwe kholo la mitundu yambiri ya anthu pamaso pa Mulungu amene iye anamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndi kuitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo. 18#Gen. 15.5Amene anakhulupirira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu, monga mwa chonenedwachi, Mbeu yako idzakhala yotere. 19#Gen. 17.17; 18.11Ndipo iye osafooka m'chikhulupiriro sanalabadira thupi lake, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, (pokhala iye ngati zaka makumi khumi), ndi mimba ya Sara idaumanso; 20ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m'chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu, 21#Gen. 18.14nakhazikikanso mumtima kuti, chimene Iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakuchichita. 22Chifukwa chake ichi chinawerengedwa kwa iye chilungamo. 23#1Ako. 10.6, 11Ndipo ichi sichinalembedwa chifukwa cha iye yekhayekha, kuti chidawerengedwa kwa iye; 24#1Ako. 10.6, 11koma chifukwa cha ifenso, kwa ife amene chidzawerengedwa kwa ife amene tikhulupirira Iye amene anaukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu, 25#Yes. 53.5-6; 1Ako. 15.17-20; 1Pet. 1.21amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama.
Currently Selected:
AROMA 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: