YouVersion Logo
Search Icon

AROMA 8

8
Moyo wathu watsopano mwa Khristu
1Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa. 2#2Ako. 3.6; Aro. 7.24-25Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa. 3#Aheb. 10.1-2, 10, 14Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi; 4kuti choikika chake cha chilamulo chikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. 5#Yoh. 3.6Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: 6#Aro. 8.13pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere. 7#Yak. 4.4Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero. 8Ndipo iwo amene ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu. 9#1Ako. 3.16; 6.19Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu. 10Ndipo ngati Khristu akhala mwa inu, thupilo ndithu lili lakufa chifukwa cha uchimo; koma mzimu uli wamoyo chifukwa cha chilungamo. 11#1Ako. 6.14Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.
Ife ndife ana a Mulungu
12Chifukwa chake, abale, ife tili amangawa si ake a thupi ai, kukhala ndi moyo monga mwa thupi; 13#Aro. 8.6; Aef. 4.22; Agal. 6.8; Akol. 3.5pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo. 14#Agal. 5.18Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu. 15#1Ako. 2.12; Agal. 4.5-6Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate! 16#Aef. 1.13Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu; 17#Mac. 26.18; Agal. 4.7; Afi. 1.29ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.
Zolengedwa zonse zilindira ana a Mulungu
18 # 2Ako. 4.17 Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife. 19#2Pet. 3.13Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. 20Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo 21kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu. 22Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano. 23#2Ako. 5.5; Luk. 20.36Ndipo si chotero chokha, koma ife tomwe, tili nazo zoundukula za Mzimu, inde ifenso tibuula m'kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo chiomboledwe cha thupi lathu. 24#Aheb. 11.1Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chioneka si chili chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya? 25Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro.
26 # Aro. 8.34; Yak. 4.3 Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka; 27#Yer. 17.10ndipo Iye amene asanthula m'mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuno cha Mulungu. 28#2Ako. 4.17Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake. 29#2Ako. 3.18; Aef. 1.5, 11; Akol. 1.15, 18; 1Pet. 1.2Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri; 30#Yoh. 17.22ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso ulemerero.
Mulungu ali nafe, adzatitsutsa ndani?
31 # Mas. 118.6 Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani? 32#Aro. 4.25Iye amene sanatimana Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye? 33#Yes. 50.8-9Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye amene awayesa olungama; 34#Yes. 50.8-9; Akol. 3.1; Aheb. 7.25ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife. 35Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Khristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsa kapena lupanga kodi? 36#Mas. 44.22Monganso kwalembedwa,
Chifukwa cha Inu tilikuphedwa dzuwa lonse;
tinayesedwa monga nkhosa zakupha.
37 # 2Ako. 2.14 Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda. 38Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, 39ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Currently Selected:

AROMA 8: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in