Lk. 16
16
Fanizo la kapitao wochenjera
1Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene anali ndi kapitao wake. Anthu adaadzamneneza kapitaoyo kuti akumwaza chuma cha mbuye wake. 2Tsono mbuye wakeyo adamuitana, namufunsa kuti, ‘Nchiyani chimene ndikumva za iwe? Undifotokozere za ukapitao wako, pakuti sungakhalenso kapitao ai.’ 3Apo kapitaoyo adayamba kuganiza mumtima mwake kuti, ‘Ndichite chiyani, popeza kuti mbuye wanga akundilanda ukapitao? Kulima, ai, ndilibe mphamvu. Kupemphapempha, ainso, kukundichititsa manyazi. 4Chabwino, tsopano ndadziŵa choti ndichite, kuti anthu akandilandire ku nyumba zao, ukapitao ukandithera.’ 5Motero adaitana angongole a mbuye wake mmodzimmodzi. Adafunsa woyamba kuti, ‘Kodi uli ndi ngongole yotani kwa mbuye wanga?’ 6Iye adati, ‘Mafuta amuyeso wokwanira mitsuko makumi khumi.’ Kapitaoyo adamuuza kuti, ‘Nayi kalata yako yangongole, khala pansi msanga, ungolembapo mitsuko makumi asanu.’ 7Adafunsanso wina kuti, ‘Nanga iwe, ngongole yako ndi yotani?’ Iye adati, ‘Tirigu wamuyeso wokwanira matumba makumi khumi.’ Kapitaoyo adamuuza kuti, ‘Nayi kalata yako yangongole, ungolembapo matumba makumi asanu ndi atatu.’ 8Apo mbuye wa kapitao wonyenga uja adamuyamikira chifukwa cha kuchenjera kwake. Pajatu pokhala ndi anzao, anthu ongokonda zapansipano ngochenjera koposa anthu okhala m'kuŵala kwa Mulungu.”
9 #
Tob. 4.9-11
Yesu popitiriza mau adati, “Ndipo Ine ndikukuuzani kuti mudzipezere abwenzi ndi chuma chonyengachi. Apo chumacho chikadzakutherani, Mulungu adzakulandirani ku nyumba zamuyaya. 10Wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ngwokhulupirikanso pa zazikulu. Ndipo wonyenga pa zazing'ono, amanyenganso pa zazikulu. 11Tsono ngati mwakhala osakhulupirika pa chuma chonyengachi, ndani nanga adzakusungizeni chuma chenicheni? 12Ndipo ngati mwakhala osakhulupirika ndi za wina, ndani adzakupatseni zimene zili zanuzanu?
13 #
Mt. 6.24
“Palibe wantchito amene angathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkunyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.”
Za Malamulo ndi Ufumu wa Mulungu
14Afarisi atamva zonsezi, adamseka Yesu, chifukwa iwo anali okonda ndalama. 15Ndipo Iye adaŵauza kuti, “Inu mumadziwonetsa olungama pamaso pa anthu, koma Mulungu amaidziŵa mitima yanu. Pajatu zimene anthu amaziyesa zamtengowapatali, m'maso mwa Mulungu zimaoneka zonyansa.
16 #
Mt. 11.12, 13 “Malamulo a Mose ndi zolemba za aneneri zinkagwirabe ntchito mpaka nthaŵi ya Yohane Mbatizi. Kuyambira pamenepo Uthenga Wabwino ukulalikidwa wakuti Mulungu akukhazikitsa ufumu wake, ndipo anthu onse akuyesetsa mwamphamvu kuloŵamo. 17#Mt. 5.18Koma nkwapafupi kuti thambo ndi dziko lapansi zithe, kupambana kuti kalemba kakang'ono ka pa Malamulo kathe mphamvu.
18 #
Mt. 5.32; 1Ako. 7.10, 11 “Aliyense amene asudzula mkazi wake, nakwatira wina, akuchita chigololo. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.”
Za munthu wachuma ndi Lazaro
19“Panali munthu wina wachuma, amene ankavala zovala zamtengowapatali, ndipo ankasangalala ndi kudyerera masiku onse. 20Panalinso munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadzagona pa khomo la munthu wachuma uja. Iyeyu anali ndi zilonda m'thupi lonse. 21Ankalakalaka kudya nyenyeswa zimene zinkagwa pansi kuchokera pa tebulo la wachuma uja. Koma si pokhapo, ngakhale agalu ankabwera kumadzanyambita zilonda zake.
22“Munthu wosauka uja adamwalira, angelo nkumunyamula, nakamtula m'manja mwa Abrahamu. Munthu wachuma uja nayenso adamwalira, naikidwa m'manda. 23#2Es. 7.36; 8.59Pamene ankazunzika ku Malo a anthu akufa, wachuma uja adayang'ana kumwamba naona Abrahamu ali patali, ndi Lazaro ali pambali pakepa. 24Pamenepo adanena mokweza mau kuti, ‘Atate Abrahamu, mundichitire chifundo. Tumani Lazaro aviike nsonga ya chala chake m'madzi kuti adzaziziritseko lilime langa, pakuti ndikuzunzika koopsa m'moto muno.’ 25Koma Abrahamu adati, ‘Mwana wanga, kumbukira kuti udalaandiriratu zokondweretsa ukadali ndi moyo, pamene Lazaro adaalandira zoŵaŵa. Koma tsopano iye akusangalala kuno, pamene iwe ukuzunzika kwambiri. 26Ndiponso pakati pa ife ndi inu pali chiphompho, kotero kuti ofuna kuchoka kuno kuwolokera kwanuko, sangathe ai. Chimodzimodzinso kuchoka kwanuko kuwolokera kuno.’
27“Apo wachuma uja adati, ‘Ndipotu ndikukupemphani atate, kuti mumtume Lazaroyo apite ku nyumba ya bambo wanga. 28Kumeneko ndili ndi abale anga asanu. Akaŵachenjeze, kuwopa kuti iwonso angabwere ku malo ano amazunzo.’ 29Koma Abrahamu adati, ‘Iwo ali ndi mabuku a Mose ndi a aneneri. Amvere zam'menemo.’ 30Iye adati, ‘Iyai, atate Abrahamu, koma wina atauka kwa akufa nkupita kwa iwo, apo adzatembenuka mtima.’ 31Koma Abrahamu adamuuza kuti, ‘Ngatitu iwo samvera Mose ndi aneneri, sangathekenso ngakhale wina auke kwa akufa.’ ”
Currently Selected:
Lk. 16: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: