Lk. 17
17
Za zochimwitsa ndi za kukhululukira
(Mt. 18.6-7, 21-22; Mk. 9.42)
1Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Zochimwitsa anthu sizingalephere kuwoneka, koma tsoka kwa munthu wobwera nazoyo. 2Kukadakhala kwabwino kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukamponya m'nyanja, kupambana kuti achimwitse mmodzi mwa ana ang'onoang'onoŵa. 3#Mt. 18.15Chenjerani tsono!
“Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire. 4Akakuchimwira kasanunkaŵiri pa tsiku, nabwera kasanunkaŵiri kudzanena kuti, ‘Pepani,’ umkhululukire ndithu.”
Za chikhulupiriro
5Atumwi adapempha Ambuye kuti, “Mutiwonjezere chikhulupiriro.” 6Koma Ambuye adati, “Mukadakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa kwambiri ngati kambeu ka mpiru, bwenzi mutauza mkuyu uwu kuti, ‘Zuka, kadzibzale m'nyanja,’ ndipo ukadakumverani ndithu.”
Za udindo wa antchito
7Yesu adatinso, “Utha kukhala ndi wantchito wolima ku munda kapena woŵeta nkhosa. Pamene iye wafika kuchokera ku munda, kodi ungamuuze kuti, ‘Bwera msanga, udzadye?’ 8Sungatero ai, koma udzamuuza kuti, ‘Konzere chakudya. Ukonzeke kunditumikira mpaka ineyo ndidye ndi kumwa. Iweyo udya ndi kumwa pambuyo pake.’ 9Kodi ungamthokoze wantchitoyo chifukwa chakuti wachita zimene unamlamula? 10Choncho inunso, mutachita zonse zimene adakulamulani, muziti, ‘Ndife antchito osayenera kulandira kanthu. Tangochita zimene tinayenera kuchita.’ ”
Yesu achiritsa akhate khumi
11Pa ulendo wake wopita ku Yerusalemu, Yesu adadzera m'malire a Samariya ndi Galileya. 12Pamene ankaloŵa m'mudzi wina, anthu khumi akhate adadzamchingamira. Adaima kutali, 13nanena mokweza mau kuti, “Yesu Ambuye, tichitireni chifundo.” 14#Lev. 14.1-32Pamene Yesu adaŵaona, adaŵauza kuti, “Pitani, kadziwonetseni kwa ansembe.” Pamene iwo ankapita, adachira.
15Tsono mmodzi mwa iwo, ataona kuti wachira, adabwerera nayamba kuyamika Mulungu mokweza mau. 16Adagwada nkuŵerama kwambiri pamaso pa Yesu, namthokoza. Koma munthuyo anali Msamariya. 17Apo Yesu adati, “Kodi achira aja si khumi? Nanga asanu ndi anai ena aja ali kuti? 18Ndiye kuti sadabwerere wina aliyense kudzayamika Mulungu, koma mlendo yekhayu?” 19Kenaka Yesu adauza munthuyo kuti, “Nyamuka, pita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”
Za m'mene Mulungu adzakhazikitsire ufumu wake
(Mt. 24.23-28, 37-41)
20Afarisi ena adafunsa Yesu kuti, “Kodi Mulungu adzakhazikitsa liti ufumu wake?” Yesu adaŵayankha kuti, “Mulungu sakhazikitsa ufumu wake mooneka ndi maso ai. 21Anthu sadzati, ‘Suuwu, uli pano,’ kapena, ‘Suuwo,’ pakuti ngakhale tsopano Mulungu akukhazikitsa ufumu wake pakati panu.”
22Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Akudza masiku pamene mudzalakalaka kuwona nthaŵi ya kudza kwa Mwana wa Munthu ngakhale tsiku limodzi lokha, koma simudzaloledwa ai. 23Anthu azidzakuuzani kuti, ‘Suuwo uli uko,’ kapena, ‘Suuwu uli pano,’ musadzapiteko kapena kuŵatsatira ai. 24Pajatu monga mphezi imang'anipa nkuŵala kuchokera mbali ina ya kuthambo kufikira mbali yake ina, Mwana wa Munthu adzateronso pa tsiku la kubwera kwake. 25Koma Iye ayenera kuti ayambe wamva zoŵaŵa zambiri, ndipo kuti anthu amakono amkane.
26 #
Gen. 6.5-8
“Monga momwe zidaachitikira pa nthaŵi ya Nowa, zidzateronso pa nthaŵi ya Mwana wa Munthu. 27#Gen. 7.6-24Masiku amenewo anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kumakwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Pamenepo chigumula chidafika nkuŵaononga onse. 28#Gen. 18.20—19.25 Monga momwe zidaachitikiranso pa nthaŵi ya Loti. Anthu ankangodya ndi kumwa, ankagulitsana malonda, ankabzala mbeu, ankamanga nyumba. 29Koma tsiku limene Loti adatuluka m'Sodomu, Mulungu adagwetsa moto ndi miyala yoyaka ya sulufule nkuŵaononga onsewo. 30Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke.
31 #
Mt. 24.17, 18; Mk. 13.15, 16 “Tsiku limenelo, amene ali pa denga, asadzatsike kukatenga katundu wake m'nyumba. Chimodzimodzinso amene ali ku munda, asadzabwerere ku nyumba. 32#Gen. 19.26 Kumbukirani za mkazi wa Loti. 33#Mt. 10.39; 16.25; Mk. 8.35; Lk. 9.24; Yoh. 12.25Aliyense woyesa kudzisungira moyo wake, adzautaya, koma woutaya adzausunga. 34Kunena zoona, usiku umenewo, padzakhala anthu aŵiri pa bedi limodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. 35Azimai aŵiri adzakhala akusinja pamodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya, 36Anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.” 37Apo ophunzira ake adamufunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti, Ambuye?” Yesu adati, “Kumene kwafera chinthu, nkumeneko kumasonkhana miphamba.”
Currently Selected:
Lk. 17: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: