Gen. 3

3
Kuchimwa kwa Munthu
1 # Lun. 2.24; Chiv. 12.9; 20.2 Njoka inali yochenjera kupambana zamoyo zonse zimene Chauta adazilenga. Njokayo idafunsa mkazi uja kuti, “Kodi nzoona kuti Mulungu adakuletsani kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse m'munda muno?” 2Mkazi uja adayankha kuti, “Tingathe kudya zipatso za mtengo uliwonse m'munda muno, 3kupatula wokhawo umene uli pakati pake. Mulungu adanena kuti tisadye zipatso za mtengo umenewo, ngakhale kuzikhudza, chifukwa choti tikadzangotero, tidzafa.” 4Koma njokayo idayankha mkaziyo kuti, “Iyai, kufa simudzafa konse. 5Mulungu amadziŵa kuti inu mukadzadya zipatso zimenezi, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala monga momwe aliri Mulunguyo. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.”#3.5: Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa: Ndiye kuti mudzadziŵa zonse. 6Tsono mkaziyo adaona kuti mtengowo ndi wokongola, ndiponso kuti zipatso zake zingakhale zokoma kudya. Pompo adayamba kukhumbira kuti adyeko zipatsozo, adzakhale wanzeru. Motero adathyolako zipatso zina za mtengowo, naadya. Tsono zina adapatsako mwamuna wake, ndipo iyenso adadya. 7Atangodya choncho, adazindikira kuti ali maliseche. Choncho adasoka masamba a mkuyu navala. 8Madzulo dzuŵa litapepa, aŵiriwo adamva mtswatswa, Chauta akuyenda m'mundamo, ndipo iwo adabisala m'katikati mwa mitengo, kuti Iye angaŵaone. 9Koma Chauta adamuitana Adamu uja kuti, “Kodi uli kuti?” 10Adamu adayankha kuti, “Ndinakumvani m'mundamu ndipo ndinaopa, ndiye ndinabisala ntaona kuti ndili maliseche.” 11Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi adakuuza ndani kuti uli maliseche? Kapena wadyatu zipatso za mtengo uja ndidakuuza kuti usadyewu eti?” 12Pamenepo Adamu adayankha kuti, “Mkazi mudandipatsayu ndiye amene anandipatsa zipatsozo kuti ndidye, ndipo ndadyadi.” 13#2Ako. 11.3; 1Tim. 2.14 Apo Chauta adafunsa mkazi kuti, “Kodi iwe, zimene wachitazi wachitiranji?” Mkazi uja adayankha kuti, “Njoka ndiyo imene inandinyenga kuti ndidye.”
Mulungu apereka chilango
14Pamenepo Chauta adauza njokayo kuti,
“Chifukwa chakuti wachita zimenezi,
ndiwe wotembereredwa
pakati pa nyama zonse za pansi pano,
zoŵeta ndi zakuthengo zomwe.
Kuyambira tsopano mpaka muyaya
udzakwaŵa ndi kumimba kwako,
ndipo chakudya chako chidzakhala fumbi.
15 # Chiv. 12.17 Ndidzaika chidani
pakati pa iwe ndi mkazi,
padzakhala chidani
pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake.
Idzaphwanya mutu wako,
ndipo iwe udzaluma chidendene chake.”
16Pambuyo pake Mulungu adauza mkaziyo kuti,
“Ndidzaonjeza zovuta zako
pamene udzakhala ndi pathupi,
udzamva zoŵaŵa
pa nthaŵi yako ya kubala mwana.
Udzakhumba mwamuna wako,
ndipo mwamuna wakoyo adzakulamulira iwe.”
17 # Ahe. 6.8 Kenaka Mulungu adauza Adamu kuti,
“Iwe unamvera mkazi wako,
wadya zipatso zija
zimene ndidaakuuza kuti usadye.
Nthaka idzatembereredwa
chifukwa cha zimene wachitazi.
Udzayenera kugwira ntchito yathukuta
nthaŵi ya moyo wako wonse,
kuti upeze chakudya chokwanira.
18M'nthakamo mudzamera zitsamba
za minga ndi za nthula,
ndipo iwe udzadya zomera zakuthengo.
19Udzayenera kukhetsa thukuta
kuti upeze chakudya,
mpaka udzabwerera kunthaka komwe udachokera.
Udachokera ku dothi,
udzabwereranso kudothi komweko.”
20Adamu#3.20: Adamu: Dzina limeneli tanthauzo lake ndiye kuti “munthu”, kapena “mtundu wa anthu”. adatcha mkazi wake Heva,#3.20: Heva: Dzina limeneli limamveka ngati mau achihebri otanthauza kuti “kukhala moyo”, amene pa mutu uno tikunena kuti “mtundu wa anthu”. Malembedwe ena “Hava”, malembedwe enanso “Eva”. chifukwa choti iyeyu anali mai wa anthu onse. 21Ndipo Chauta adasokera Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa naŵaveka onse aŵiriwo.
Adamu ndi Heva atulutsidwa m'munda
22 # Chiv. 22.14 Chauta adati, “Tsopano munthuyu wakhala monga tiliri ife, popeza kuti akudziŵa zabwino ndi zoipa. Asaloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyowo ndi kukhala moyo mpaka muyaya.” 23Motero Chauta adamtulutsamo m'munda mwa Edeni muja, kuti azilima m'nthaka momwe adachokera. 24Atampirikitsira kunja Adamuyo, Mulungu adaika akerubi kuvuma kwa munda wa Edeni. Adaikanso lupanga lamoto limene linkazungulira mbali zonse, kutchinjiriza mtengo wopatsa moyo uja, kuti wina asaufike pafupi.

S'ha seleccionat:

Gen. 3: BLY-DC

Subratllat

Comparteix

Copia

None

Vols que els teus subratllats es desin a tots els teus dispositius? Registra't o inicia sessió